ChichewaNkhani

‘JB asabisalire kwa amphawi za kuyenda’

Pambali poyenda kunja, Banda akukhaliranso kugawa ng'ombe, nyumba ndi kukweza mafumu
Pambali poyenda kunja, Banda akukhaliranso kugawa ng’ombe, nyumba ndi kukweza mafumu

Mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda wamenyetsa nkhwangwa pamwala ponena kuti, zivute zitani, sangasiye kuyendera anthu m’midzimu ndipo wati zikafika povutitsitsa atha kukwera ‘kabaza’. Koma ena mwa anthu omwe athirapo ndemanga pa mawu a mtsogoleriyu, kuphatikizapo akuluakulu ena odziwa za mmene chuma cha boma chukuyendera, apempha mtsogoleriyu kuti asinthe maganizo.

Loweruka lapita Banda adauza anthu pabwalo la Kalambo mumzinda wa Lilongwe kuti sasiya kuyendayenda chifukwa ndiyo njira yomwe akuthandizira anthu akumudzi.

Iye adati ngati pathine azikwera kabaza (njinga ya hayala) kuti afikire ‘abale ake’ ovutika. Izi zikutsutsana ndi zomwe boma lake, kudzera mwa nduna ya zachuma Maxwell Mkwezalamba, lidalengeza kuti layamba laimitsa kaye maulendo a nduna, akukuakulu ogwira ntchito m’boma, kuphatikizapo Pulezidenti, kuti mwina chuma cha boma chingabwerere m’chimake.

Bungwe la Catholic Commission for Justice and Peace (CCJP) sabata yatha lidadandaula ndi maulendo a mtsogoleriyu ponena kuti ndi njira imodzi yowonongera  chuma cha dziko lino. Bungweli lidati pamene Pulezidentiyu wayenda m’dziko mommuno akumaononga K10 miliyoni patsiku.

Koma mneneri wa boma, Brown Mpinganjira, akuti sakudziwa ndalama zomwe zikuwonongeka koma adati atiuzabe pambuyo pa kukumana ndi akuluakulu a zachuma.

Ngatidi ndi zoona kuti ulendo wa Pulezidenti woyendera anthu ake m’dziko mom’muno umadya ndalama zokwana K10 miliyoni patsiku, atati azigwiritse ntchito ina, ikhoza kuthandiza pachitukuko chomwe chingapindulire anthu ochuluka.

Mwachitsanzo, m’ndondomeko ya zachuma cha boma ya 2013/2014, boma lidapatula K7 miliyoni n’kuika mthumba la Local Development Fund (LDF) zothandizira pantchito ya chitukuko cha m’midzi m’dera la phungu mmodzi pachaka.

Mwezi wa October wokha, pali umboni woti mtsogoleriyu adachititsa misonkhano yosachepera 17 m’dziko muno.

Nduna ikaperekeza mtsogoleriyu imalandira K45 000 patsiku ngati alawansi; wachiwiri kwa nduna amalandira K39 600; wothandizira nduna K15 000; madalaivala ndi achitetezo amapindira m’thumba K6 000, malinga ndi malipiro amamulumuzanawa amene adaunikidwanso mu November 2012. Malipirowa amagunda papakulu ngati zochitikazo zikuchitikira kunja kwa Lilongwe.

Lachiwiri lapitali, anthu a m’midzi ya Chamba, Msanganiza, Khunju, Kamtukule, Jiya, ndi ina kwa Senior Chief Somba m’boma la Blantyre adauza Tamvani kuti iwo ali pamoto chifukwa cha kusowa kwa chimanga, feteleza wa makuponi komanso mankhwala m’zipatala.

Anthu ena amene adalankhula ndi Tamvani tidawapeza atagona pa Admarc ya Mbame, pomwe ankadikirira chimanga ndi feteleza.

Mmodzi mwa anthuwo, Ephraim Kabichi, wa m’mudzi mwa Kamtukule, adati: “Anthu atha kusangalala pamene mtsogoleriyu wayenda koma amene akuthandizika ndi ochepa. Ndalama zikugwiritsidwa ntchitozo ndi zambiri zomwe zikadapindulira anthu ambiri.

“Sabata ino ndi yachitatu sindidagule feteleza, feteleza adangobwera kamodzi kokha. Kuchipatala kulibe mankhwala komanso chimanga chidasowa kalekale kuno. Ndalamayo itha kuthandiza anthu tonse kuno.”

Mkulu wa bungwe loona momwe nkhani zachuma zikuyendera la Malawi Economic Justice Network (Mejn), Dalitso Kubalasa, wati Pulezidenti Banda akungobisala pachipande.

“Ndalamazo zithanso kuposa K10 miliyoni pamene wayenda. Koma ndalama zimenezi zikuthandiza anthu angati? Ngati dziko tione zimenezi.

“Tili ndi mavuto ambiri monga kusowa mankhwala m’zipatala komanso momwe chuma chathu chilili,” adatero Kubalasa, n’kuonjezera kuti izi zikuchitika pamene chaka chamawa dziko lino lili  ndi chisankho ndiye n’zosakaikitsa kuti cholinga cha maulendowo ndi ndale zokopa anthu kuti adzavotere mtsogoleriyu ndi chipani chake cha PP, osati kuti anthu akumudzi ndiwo akupindula nawo.”

Katakwe pandale Blessings Chinsinga akuti Nyumba ya Malamulo ndiyo ingathane ndi kuyendayenda kwa Banda.

“Kodi ndalama zimenezi akuzitenga kuti? Kuti mufunse yankho likhala loti zikuchokera m’ndondomeko yomwe idavomerezedwanso ndi Nyumba ya Malamulo. Ndiye tikuyenera kuona bwino ndalama zomwe zikupita kuthumba lomwe mtsogoleri azigwiritsira ntchito,” adatero Chinsinga.

Sabata yatha, bungwe la CCJP lidauza atolankhani kuti lakwiya ndi maulendo a Banda ogawa ng’ombe ndi kukweza mafumu chifukwa akumaononga zambiri kwa anthu ochepa.

“Ndi zosamveka kuti boma liziononga K10 miliyoni pokagawa ng’ombe ziwiri za ndalama pafupifupi K400 000. Mtsogoleri asiyire ntchitoyi kwa akuluakulu a kuunduna wa zamalimidwe,” adatero mlembi wa bungweli Peter Chinoko.

Banda adati maulendowa azichitikabe chifukwa panganolo likuloleza maulendo ofunika okha.

Related Articles

Back to top button