Chichewa

‘Kudali ku Namiwawa CDSS’

Listen to this article
Akuphika chimbale: Chimbalanga
Akuphika chimbale: Chimbalanga

DJ Khumbo ndi mmodzi mwa anyamata odziwika bwino pankhani yotembenuza zimbale kuti anthu azivina. Iye amatembenuza zimbale monga DJ ndi 4Tees Disco imene amayenda nayo ndi gulu la msangulutso la Jai Banda la Entertainers Promotions.

Kusakaniza nyimbo tsopano kufika pena, pamene DJ Khumbo, yemwe dzina lake lenileni ndi Khumbo Nyirenda, akhale akutengana ndi Bernadette Uzamba. Lero kuli bridal shower ku Village House, kwa Manase mumzinda wa Blantyre ndipo Loweruka likudzali, awiriwo adzamangitsa ukwati wawo ku St James CCAP asanasunthe kupita kuholo ya sukulu ya sekondale ya Zingwangwa komwe kukakhale madyerero.

Kodi awiriwo adakumana bwanji?

“Tinkaphunzira limodzi kusukulu ya Namiwawa CDSS. Nthawiyo ndinkakhala ku Mbayani pomwe Berna ankakhala kwa Manase. Ndidazunzika kuti andilole. Tidali kalasi imodzi,” adatero Khumbo.

Ena n’kumaganiza kuti icho chidali chibwana chabe, koma Khumbo adati adalimba mtima ndipo adalimbikira kufunsira Bernadetta mpaka adatheka mu 2005.

Bernadette akuti ankakana mpaka materemu awiri kutha chifukwa sankatsimikiza kuti Khumbo akukonza zazikulu.

“Padali povuta kungomulola nthawi yomweyo chifukwa tidali pasukulu. Koma nditaona kuti akuzama, ndidathyola khosi,” adatero iye.

Khumbo akuti achinyamata ayenera kudekha asanapeze womanga naye banja, koma akaona kuti ayanjana ndi wina, asachedwe. Pajatu mtima wa moto sudziwika, umangofunika kuti pamene papsa utonoreretu.

“Sikukongola kokha kudanditenga mtima mwa Berna. Iye ali ndi khalidwe labwino. Takhala tikukhalira limodzi kwa zaka zingapo ndipo tsopano tafuna tikadalitse ukwati wathu,” adatero iye.

Akumwetulira, Bernadette adati: “Asungwana ayenera kufatsa asanapeze mwamuna. Masiku ano kuli amuna anjomba. Nchapamwamba kupeza mwamuna wonga Khumbo,” adatero iye.

Khumbo ndi mzime m’banja la ana anayi ndipo amachokera ku Ezondweni, kwa Senior Chief Mtwalo m’boma la Mzimba pamene Bernadette ndi wachiwiri kubadwa m’banja la ananso anayi ndipo kwawo ndi kwa Chipembwere, T/A Mabuka ku Mulanje.

Related Articles

Chichewa

‘Kudali ku Namiwawa CDSS’

Listen to this article
Khumbo, Bernadette ndi mwana wawo

Check Also
Close
Back to top button
Translate »