Nkhani

‘Lamulo la chuma cha pulezidenti liunikidwenso’

Mmodzi mwa akatswiri a za malamulo Edge Kanyongolo wati lamulo lomwe likukamba za katundu ndi chuma cha atsogoleri a dziko liunikidwenso ndi cholinga chopatsa mphamvu zochuluka kwa Amalawi akafuna kufufuza atsogoleri omwe akugwiritsa ntchito maudindo awo podzikundikira chuma.

Izi zadza pamene dziko la Malawi ladzidzimuka ndi kuchuluka kwa chuma cha mtsogoleri wakale wa dziko lino malemu Bingu wa Mutharika ngakhale kuti adakhala pampandowu kwa kanthawi kochepa.

Kwa zaka 8 zokha zimene Mutharika adakhala pulezidenti wa dziko lino, chuma chake chidawonjezekera modabwitsa kuchoka pa K150 miliyoni panthawi imene asankidwa kukhaka pulezidenti kufika pa K61 biliyoni mmene ankamwalira, zomwe Amalawi ambiri akuti zachulukitsa poyerekeza malipiro amene mtsogoleri wa dziko amalandira pamwezi.

Malamulo a dziko lino amafotokoza kuti Pulezidenti ndi wachiwiri wake sakuyenera kudulidwa msonkho pamalipiro awo apamwezi. Kuphatikiza apo, ndi misonkho ya anthu osauka, atsogoleriwa amakhala ndi bajeti yogulira chakudya komanso ziwiya za m’nyumba zawo.

Pakatha zaka zisanu zilizonse, atsogoleriwa alinso ndi ufulu woitanitsa kuchokera kunja galimoto imodzi ya kumtima kwawo popanda kupereka msonkho wotchedwa ‘Duty’ ku bungwe lotolera msonkho la Malawi Revenue Authotiry (MRA).

Kwa nthawi yaitali, atsogoleri ena akhala akugwiritsa ntchito mphamvu ndi ufulu umene lamulo limawapatsa poitanitsa katundu wochitira bizinesi zosiyanasiyana koma osapereka msonkho ku MRA, zomwe zikutsutsana ndi malamulo a dziko lino.

Pofuna kuthana ndi mchitidwewu, boma lidakhazikitsa bungwe lapadera la Special Law Commission (SLC) m’chaka cha 2006 ndi cholinga choti liunikenso bwino gawo 88 la malamulo a dziko lino.

Ntchito yake yaikulu inali kukonza lamulo lokakamiza Pulezidenti, nduna komanso akuluakulu ena ogwira ntchito m’boma kunena poyera mmene chuma chawo chilili asanalumbiritsidwe pamaudindo osiyanasiyana.

Kafukufuku wa bungweli adasonyeza kuti kupatula lamulo lokakamiza atsogoleri kubwera poyera pakatundu yemwe ali nawo, maiko monga Uganda, Kenya ndi Tanzania adaikanso ndondomeko ndi mfundo zowonjezera zothandiza munthu akafuna kudziwa kapena kutsatira momwe chuma cha atsogoleri awo chikuchulukira kudzera mumaudindo awo ngati pulezidenti, nduna kapena phungu wa Nyumba ya Malamulo.

Mwa mfundo zina, bungweli lidavomereza kuti munthu wogwira ntchito m’boma sakuyenera kugwiritsa ntchito udindo wake podzikundikira yekha chuma kapena anzake; asagwirenso ntchito zina kupatula yomwe adalembedwa ndi boma; apewe kugwira ntchito zomwe sizikugwirizana ndi udindo wake komanso asagwiritse ntchito udindo wake kapena katundu wa boma molakwika.

Ngakhale izi zili choncho, zikuwoneka ngati Amalawi alibe mphamvu komanso lamulo lomwe lingawaikire kumbuyo akafuna kulondoloza chuma cha atsogoleri awo. Izi zikupereka mwayi kwa atsogoleriwa kugwiritsa ntchito maudindo awo momwe angafunire popanda wina kuwafunsa.

Kanyongolo adati izi zikusonyeza kufooka kwa malamulo a dziko lino n’chifukwa chake atsogoleri akutengerapo mwayi.

Iye adati lamulo lokhudza katundu ndi chuma cha Pulezidenti, wachiwiri wake ndi nduna za boma ndi lokwanira, koma likusowekera nsanamira zake zimene anthu wamba angagwiritse ntchito polondoloza chumacho.

Mkuluyu adafotokoza kuti poonjezera lamulo limene lilipo kale, Nyumba ya Malamulo iganizirenso zokhazikitsa lamulo lina lokakamiza atsogoleri kubweranso poyera ndi chuma chimene apeza pamene akuchoka m’maudindo awo.

Kanyongolo akuti akadakonda mabungwe a Financial Intelligence Unit (FIU) ndi Malawi Revenue Authority (MRA) atapatsidwa mphamvu zounika mmene chuma cha atsogoleri chilili pamiyezi inayi iliyonse kapena pakutha pa chaka kuti Amalawi azidziwa ngati atsogoleriwa sakugwiritsa ntchito maudindo awo molakwika.

“Ndikunena izi chifukwa chipanda nkhani ya msonkho womwe mtsogoleri wakaleyu sanapereke ku MRA, dziko lino silikadadziwa kuti a Mutharika anali wolemera chonchi,” Kanyongolo adatero.

Katswiri wina pa zamalamulo, Justin Dzonzi, wati gawo 88 la malamulo a dziko ndi lopanda ntchito chifukwa silikupatsa mphamvu ndi chitetezo kwa nzika imene ikufuna kulondoloza momwe chuma cha atsogoleri chilili.

Dzonzi adati ku Uganda nzika zili ndi mphamvu zofufuza atsogoleri awo mmene akugwiritsira ntchito udindo wawo komanso chuma cha boma.

Koma mkulu wa bungwe la owerengera ndalama la Society of Accountants in Malawi (Socam) Evelyn Mwapasa akuti Amalawi atha kulondoloza katundu wa atsogoleri awo kudzera m’makalata ndi mapepala okhudzana ndi misonkho kuchokera ku MRA.

Koma Mwapasa adatsindika kuti vuto lalikulu m’dziko muno ndi kasungidwe ka mafayilo okhudzana ndi misonkho.

“M’maiko ena, munthu sungapikisane nawo pampando wa pulezidenti kapena phungu wa ku Nyumba ya Malamulo pokhapokha utatulutsa umboni wosonyeza kuti umalipira msonkho,” Mwapasa adatero.

Iye adati pofuna kuthetsa katangale, bungwe lotolera msonkho liyenera kulimbikitsa ntchito yosunga mafayilo a misonkho.

“Ndipo akaona kuti atsogoleri athu akulemera modabwitsa, MRA ikuyenera kufufuza ndi cholinga choti wina asamadyere masuku pamutu Amalawi osauka,” Mwapasa adatsindika.

Mkulu wa Consumers Association of Malawi (Cama) John Kapito wapempha Amalawi kuti asataye nthawi kulimbana ndi chuma chimene Mutharika adazikundikira.

Mmalo mwake, Kapito adati anthu akuyenera kukhala tcheru ndi boma la People’s Party (PP) womwe akuti uli ndi kuthekera kowononga chuma chambiri ngati sipangapezeke njira zolitchingira.

“Si zodabwitsa kuti malemu Mutharika adapeza chuma chochuluka motere. Ifeyo ndi amene takhala tikumenya nkhondo yokakamiza atsogoleri kuti aulule chuma chawo, koma mmalo motithandiza pankhondoyi, tikutanganidwa ndi zinthu zina zopanda pake,” iye adatero.

Related Articles

Check Also
Close
Back to top button