Editors Pick

‘Samalani ndi mitengo ina’

Listen to this article
Bluegum ngati uyu siofunika kubzalidwa m’munda
Bluegum ngati uyu siofunika kubzalidwa m’munda

Kadaulo achenjeza zobzala bluegum, malaina m’munda

Katswiri wa zakasamalidwe ka nthaka m’boma la Lilongwe, Edson Chagunda, wati alimi akuyenera kusankha mitengo yobzala m’munda pofuna kuthana ndi mavuto a kuonongeka kwa nthaka.

Polankhula mwapadera ndi Uchikumbe, Chagunda adati pali mitengo ina yomwe imaononga nthaka komanso kumwa madzi omwe mbewu zikadagwiritsa ntchito ndi kukula bwino.

Iye wati mitengo monga bluegum ndi malayina ndi yoipa kunthaka ndipo ngati m’munda muli mitengo yotere mbewu sizichita bwino komanso pang’onopang’ono nthaka imaferatu.

“Mitengoyi ndi yabwino pa ntchito zina monga nkhuni ndi kupala matabwa koma vuto ndi kuononga nthaka. Masamba a mtengo wa bluegum akamaolerana amatulutsa madzi oipa omwe amapha tizilombo ting’onoting’ono ta m’nthaka.

“Vutoli limabweranso ndi zibalobalo za malayina zomwe zimatulutsa madzi oipa zikamaola ndiye tizilombo tam’nthakato tikafa nkovuta manyowa kupangika m’nthaka chifukwa ndi tomwe timaoletsa zinyalala.

“Kumbali ina, bluegum amayamwa madzi kwambiri munthaka ndiye pafupipafupi m’munda mumakhala mouma, mbewu nkumakula monyozoloka chifukwa ngakhale mukhale chonde chambiri sichingagwire ntchito bwino popanda madzi,” adatero Chagunda.

Iye wati m’malo mwa mitengo ngati imeneyi alimi akhoza kubzala mitengo yobweretsa chonde monga msangu ndi mthethe yomwe imathandiza kuonjezera chakudya cha mbewu.

“Mitengo monga mthethe ndi msangu imakoka chakudya chomwe chidalowerera pansi kwambiri ndi kuchisunga m’masamba ake ndiye masamba aja akamayoyoka ndi kumaola chakudya chija chimatsalira m’nthaka chonde ndikumabwerera,” adatero iye.

Katswiriyu wati alimi akhoza kupeza mbewu ya mitengo yovomerezekayi kwa alimi anzawo omwe ali nayo kale m’minda mwawo komanso akhoza kukatenga mbewuyi ku ofesi yoyang’anira za nthaka ndi chilengedwe ya Land Resource and Conservation Department.

Mkulu wa za malimidwe m’boma la Lilongwe Hastings Yotamu wati njira ina yotetezera nthaka ndi chonde ndi kuphimbira nthakayo ndi zinyatsi kapena mapesi kuti madzi azikhalitsamo komanso isamauluke ndi mphepo.

Yotamu wati pounda mizere, mlimi amayenera kuona mmene mtsetse wa pamalo akewo wayendera ndi kuunda mizere yopingasa mtsetsewo ndipo ngati malo ake ndi otsetsereka kwambiri ayenera kukumbuka kuika migula kuti madzi asamathamange kwambiri.

Related Articles

Back to top button