Nkhani

40 awaganizira kugwa m’ndenge yamatsenga

Listen to this article

Anthu 40 m’boma la Ntchisi akuwaganizira kuti adagwa m’ndege yamatsenga yomwe anthuwo adakwera akuchokera kotamba.

Nkhaniyi idadzidzimutsa anthu ambiri okhala m’mudzi mwa Chikuta m’dera la mfumu yaikulu Chilooko m’bomali Lachitatu pa 17 August pomwe chinthu china chachilendo, chomwe akuchiganizira kuti ndi ndege ya ufiti, chidagwa m’mudzimo.

Phiri: Nayi ndenge ya matsenga
Phiri: Nayi ndenge ya matsenga

Malingana ndi sing’anga Pilirani Phiri wa m’mudzi mwa Ziwanda m’dera la

tidaitenga pamodzi ndi amfumu a m’mudzimo n’kupita nayo kupolisi ya Kamsonga komwe ndipo apolisi adatiuza kuti, ngati sing’anga, ine ndi amene ndingathe kuononga ndegeyo ndipodi ndidakaonongadi poitentha,’’ adatero Phiri.

Titamfunsa kuti adadziwa bwanji kuti m’ndegemo mudali anthu 40, Phiri adati adaunika ndi galasi lake lomwe amaonera zamatsenga ndipo onse amene adali mmenemo akuwadziwa ndipo achikhala kuti boma limavomereza bwenzi akuluakuluwo atawatumizira “nuclear” kuti akhaule chifukwa akumaphunzitsa ana ufiti “koma ndikatero ndiye kuti ndiika miyoyo ya makolo a anawo pachiopsezo chifukwa abale a mfitizo akhoza kukawachita chipongwe”.

“Ngakhale ena akuti ufiti kulibe, kunja kuno kukuchitika zoopsa ndipo zimatengera sing’anga amene adazama kuti adziwe zomwe zikuchitika,” adatero sing’angayo.

Mkulu wa polisi pa Kamsonga Police Unit, Inspector Kennedy Kwalira, adatsimikiza za nkhaniyi.

Iye adati nkhaniyi adailandiladi ndipo ngati apolisi sakanatha kutengapo gawo pankhaniyo koma kuuza sing’angayo kuti ndi amene adakatha kuononga ndegeyo chifukwa malamulo a dziko lino savomereza kuti kunja kuno kuli ufiti.

Related Articles

Back to top button
Translate »