Nkhani

‘Uhule wanyanya’

Listen to this article

Lero pa 1 Disembala ndi tsiku limene maiko onse padziko lapansi amakumbukira za nkhondo yolimbana ndi matenda a Edzi. Koma ngati zimene zikuchitika ku Mponela m’boma la Dowa zingapitirire, nkhondo yothana ndi matendawa ivutirapo.

Kumeneko, asungwana achichepere a zaka za pakati pa 10 ndi 14 akuti alusa kwambiri ndi mchitidwe woyendayenda m’malo omwera mowa momwe akumachita zachisembwere ndi abambo akuluakulu kuti apeze ndalama.

Polankhula pamsonkhano wothana ndi kukwatiritsa ana msanga umene adakonza a bungwe la Everychild sabata yatha, T/A Dzoole yam’bomalo yati asungwanawa amachokera m’midzi yozungulira pa Mponela omwe amathawa umphawi kwawo ndipo mfumuyo yapempha apolisi kuti achitepo kanthu pa mchitidwewu.

Iye wati asungwana osakwanitsa zaka 15 akumapezeka m’malo omwera mowa ndi ogona alendo kufunafuna abambo oti azichita nawo zachiwerewere posinthanitsa ndi ndalama kapena zinthu zina.

“Ndakumanapo kangapo ndi ana achichepere makamaka asungwana azaka za pakati pa 10 ndi 14 omwe amagulitsa matupi awo kwa abambo akuluakulu. Mchitidwewu wafika ponyanya kwambiri moti pakufunika njira youthetsera msangamsanga,” idatero mfumuyo.

Iye adati apolisi akadayesetsa kuchitapo kanthu chifukwa izi zikupangitsa kuti matenda a Edzi asathe komanso zikuchulukitsa chiwerengero cha ana osowa chithandizo cha makolo chifukwa asungwana oterewa akatenga pathupi amangobereka mwana n’kumuthawa,” adatero Dzoole.

Chiwelewele chomwe chimakhudzana kwa mbiri ndi mchitidwe wa uhule ndi njira ayayikulu yomwe imafalitsa matenda a Edzi omwe dziko lonse lapansi likukumbukira lelo. Chikalata chomwe adatulutsa a bungwe la World Health Organisation mu 2011chimasonyeza kuti anthu oposa 34.2 million dziko lonse ali ndi kachilombo ka HIV.

Wachiwiri kwa mkulu wa polisi ya Mponela George Ntetemela adatsimikiza za kukula kwa m’chitidwe wa uhule m’deralo ndipo adati apolisi ali kale pa kalikiliki kusaka njira zochotsera asungwana achichepere m’malo omwera mowa.

“Cholinga chathu sikumanga munthu koma tikufuna tiwagwire asungwana oterewa kenako tiitane makolo awo kuti tikambirane nawo,” adatero Ntetemela.

Oimira bungwe la Everychild, Tissie Msonkho, adati asungwana ambiri m’dziko muno akumalowa m’banja zaka zoyenerera zisanakwane zomwe zimapangitsa kuti azizunzika.

Msonkho anati maukwati ambiri aana achichepele amapangidwa chifukwa cha umphawi, miyambo komanso nkhanza zomwe ana maka asungwana amakumana nazo m’manyumba momwe amakhala.

Related Articles

Back to top button
Translate »