Nkhani

A ku Mozambique akulembetsa mavoti

Listen to this article
Mwafulirwa: Ndi mlandu waukulu
Mwafulirwa: Ndi mlandu waukulu

Nzika zina za m’dziko la Mozambique  zikulembetsa nawo m’kaundula wa mavoti ku Dedza popofuna kuti zidzavote nawo pa  chisankho cha magawo atatu chomwe chilipo pa 20 May, 2014.

Mneneri wa polisi ku Dedza Edward  Kabango wati panopa apolisi anjatapo kale nzika imodzi ya dzikokolo, Edward  Tenganibwino, wa zaka 28, wochokera m’mudzi mwa Golong’ozo yemwe amafuna  kulembetsa m’kaundulayu mwachinyengo.

Kabango wati Tenganibwino adanamiza  akalaliki ochita kalemberayu kuti ndi Mmalawi ndipo amachokera m’mudzi mwa  Katsekaminga ku Dedzako koma akalalikiwo adamuzindikira msanga ndi kumuneneza  kupolisi.

Bungwe logwira ntchito zophunzitsa anthu  la National Initiative for Civic Education (Nice) lati nzika zambiri za ku  Mozambique zalowa m’dziko muno kufuna kudzalembetsa nawo koma zina zidabwezedwa  akalaliki a kalemberayu atazitulukira.

Mkulu woyendetsa za maphunziro  kubungweli, Patrick Siwinda, wauza Tamvani kuti asanu agwidwapo kale koma ena  akadali zungulizunguli m’bomalo kuyesayesa kuti alembetse  m’kaundulayu.

Iye wati ambiri mwa anthuwa akuti  amafuna ziphaso zoponyera voti ndi cholinga choti azidzatha kutenga ngongole  zotukulira ulimi wa kachewere kumabanki a m’dziko muno.

Siwinda wati ambiri mwa anthu  achinyengowa akumagwiritsa ntchito ziphaso zolowera ndi kutuluka m’dziko za  Malawi komanso ziphaso zoponyera voti za m’ndondomeko ya chisankho cha chaka cha  2009 ngati umboni kuti awalembe.

“Pa 2 November, bambo wina wa ku  Mozambique adabwera ndi chiphaso cha ku Malawi kuti alembetse koma adabwezedwa,”  adatero Siwinda.

Iye adati nthumwi za bungweli zati  mchitidwewu ukuoneka m’malo olembetserako 13 a m’dera la Bembeke.

Siwinda wati madera omwe akukhudzidwa  ndi mchitidwewu ndi Katsekaminga CDSS, Mazanjala, sukulu zapulayimale za Kapesi  ndi Magaleta, sukulu zasekondale za Umbwi, Msambiro, Dedza Muslim Jamat, sukulu  ya asungwana Achisilamu ya Dedza, Dedza CCAP, Dedza LEA, Dedza Community Hall  ndi mudzi wa Dauya.

Bungwe loyendetsa zisankho m’dziko muno  la Malawi Electoral Commission

(MEC) lati mchitidwe wolembetsa kapena  kuthandizira munthu yemwe sali woyenera kulembetsa kuti alembetse ndi mlandu  waukulu ndipo wolakwa akhoza kunjatidwa.

Wofalitsa nkhani m’bungweli Sangwani  Mwafulira wati pofuna kuchepetsa mchitidwewu, zipani ndi mabungwe azisankha  oyang’anira ndondomeko ya chisankho (monitors) kuchokera m’dera lomwe  kukuchitikira ntchitoyi kuti azitha kuzindikira anthu ofuna kuchita  zachinyengo.

“Ndi bwino kusankha nthumwi za m’dera  lomwe kukugwiridwira ntchitoyi chifukwa sizivuta kuzindikira anthu. Komanso  anthu akuyenera kuzindikira kuti kuperekera umboni wabodza kuti munthu ndi  Mmalawi pomwe si Mmalawi woyenera kulembetsa m’kaundula ndi mlandu waukulu woti  munthu akhoza kulipira ndalama zokwana K500, 000 kapena kukakhala kundende zaka  ziwiri,” watero Mwafulirwa.

Related Articles

Back to top button