Chichewa

Abusa ku HIH ndi zina

 

Tsikulo ndidali pa Wenela kuitanira minibasi monga mwanthawi zonse.

“Ndirande iyi! Machinjiri iyo! A Lilongwe achamba atatu iyo yopita! Ndati achangu atatu a Lilongwe iyi!” Mukudziwa kale.

toon

Nthawi imeneyo nkuti ndikumveratu nyimbo zatsopano zokhazokha, ma headphone ali kukhutu. Pamaphulikatu nyimbo zongomasula kumene: Namadingo adabwera ndi Msati Mseke, Wambali amvekere Asungwana a kwa Chitedze, anyamata a ku Chileka akuti Mr Bossman ndipo Lucius akuti Walema. Osaiwala munthu wamkulu Nkasa akufwamphula Anenere.

Ndidachotsa ma headphone mkulu wina atandikodola. Iyetu adali atangotsika basi ndipo ndidadziwiratu kuti ndi mbusa.

Musandifunse kuti ndidadziwa bwanji chifukwa sindikuyankhani. Ndipo n’kakuuzani kuti ndidaonera mwinjiro wake wakuda, ndi kolala yoyera muchitapo chiyani? Nanga n’kakuuzaninso kuti simukudziwa kolala yoyerayi idabwera bwanji mulephera kuyankha.

Ndangokhala muno muliyenda kuchoka kwathu kwa Kanduku komwe ndidasiya mkazi wanga wokondeka, Nambe, koma ndimadziwa kuti nthawi imeneyo abusa ankaphedwa pochekedwa makosi. Iyitu idali nthawi yowawitsa pamene kukhala mbusa chidali chinthu choopsa zedi. Komatu abusa anthawiyo adali olimba mtima ndipo adayamba kuika kolala yoyera pakhosi kuti langa ndi limeneli liduleni koma sindisiya kufalitsa uthenga wabwino, kuthandiza kuti ochimwa asinthe ndipo iwo ali olungama apitirize kutero.

Ameni?

“Atsogoleri, inetu wanga ndi wa ku HIH, ndikwere ya chiyani?” adandifunsa.

“Ya Ndirande, kapena ya Machinjiri. Kwerani iyi abusa. Ya Machinjiri ndi K200, ya Ndirande K100. Simufuna bodyguard? Ndikumvatu kwaterera,” ndidatero.

Adangoseka, uku akukwera minibasi ya Ndirande. Akukwera, ndidaona chisenga chikusuzumira.

Madzulo a tsikulo, tili malo aja timakonda pa Wenela, adatulukira Abiti Patuma ali wefuwefu.

“Mkulu wina wandilipirira kuti ndipeze chitupa choyendetsera galimoto. Koma eeeh! Abale ku Ginnery Corner uku kuli gahena ndithu. Kudikira tsiku lonse uli chiimirire koma chitupa osatuluka,” adalira.

“Bwanjinso nanga?” ndidafunsa.

“Kuli mazunzo. Ena akundiuza ayendera masiku 8 nkhani yomweyi. Ukapolotu uwu. Tsono nthawi yotakata m’taunimu ikhalapo? Ndalama zopereka ndiye simasewera. Akatolera ndalamazo ndiye basi kususa kukhalepo. Osololawo aiwala kuti lero Adona Hilida athawa pano pa Wenela kuopa kukwizingidwa poti ena akuti akukhudzidwa ndi kusolola mopanda manyazi kudagundika ku Kapitolo,” adatero Abiti Patuma.

Palibe icho ndidatolapo.

“Mwati chiyani?” adafunsa wapamalopo, Gervazzio.

“Kodi simunamve kuti Mani Rich alembera akatalangwe ena kuti Adona Hilida akusautsidwa m’maganizo ndi anthu amene akusaka moyo wawo? Nanga simunamvenso kuti uja wa mabasi Leo wachita muja adachitira Pitapo, kunena kuti Adona Hilida ndiwo adawatuma kusolola khobidi?” adayankha Abiti Patuma.

Tonse tidangoti kukamwa yasaa! Man Rich amafatsa!

Atatsegula wailesi Gervazzio, tidangomva mkulu uja adawerenga kwambiri vesi yaifupi m’baibulo akulankhula. Mwamuiwala kale mkuluyu? Nanga ndichite kukuuzani za vesi ija imati Yesu analira? Kapena mwamuiwala mkulu woyang’anira maula adalira pomwe adanena kuti Moya Pete ndi Dizilo Petulo Palibe ndiwo akadaulo pobera maula?

“Amene apambana ndi Dizilo Petulo Palibe, Ukafuna Dilu Fatsa komanso Male Chauvinist Pigs,” adatero mkuluyo.

Posakhalitsa adatulukira Kenny Foot Soldier Nsongo. “Atiberanso maula. Panalibe chilungamo pamaula amenewa. Pali kukondera,” adali kutero.

“Shhhhh! Tikumvera nkhani. Mipingo ina idzatha ngati makatani,” adatero Abiti Patuma.

Gwira bango, mwaiwe, madzi akutenga!n

Related Articles

Back to top button