Chichewa

Achenjeza zobzala chinangwa cha matenda

Listen to this article

 

Katswiri oona za tizilombo toononga komanso toyambitsa matenda ku mbewu wa kunthambi ya kafukufuku ya Bvumbwe Research Station, Dr Donald Kachigamba, wati alimi apewe kubzala mbewu ya chinangwa chomwe chikuonetsa zizindikiro za matenda.

Pamene mvula ikugwa ndipo Madera ena imagwa mocheperako, alimi ena padakalipano ali pa kalikiliki kubzala mbewuyi kuti adzapeze chakudya ngakhalenso kugulitsa.

Kachigamba adati matenda a chinangwa omwe azunguza kwambiri m’maiko ambiri a mu Africa kuphatikizapo Malawi ndi a khate (cassava mosaic) komanso oola (cassava brown streak).

“Matenda a khate amapangitsa masamba a chinangwa kukwinyana pomwe matenda a kuola amapangitsa mtengo wa chinangwa kuoneka okandikakandika komanso chinangwa chenichenicho chimaola mkati mwake,” adatero katswiriyu.

Khate la chinangwa limachititsa masamba kukwinyika

Iye adalangizanso kuti ngati mbewu zina zayamba kuonetsa zizindikirozi pamene zili m’munda, mlimi akuyenera kuzizula ndi kuzitaya zikadali zazing’ono kuti zisakhale gwero la matendawa ku mbewu zina.

Katswiriyu adaonjeza kuti kachilombo kotchedwa gulugufe oyera ndi komwe kamafalitsa matendawa mmunda wa chinangwa.

“Gulugufeyu payekha sioopsa koma kuipa kwake ndi kwakuti amafalitsa matendawa m’munda wa chinangwa choncho chofunika ndi kungoonesetsa kuti mmunda mulibe matenda,” adatero katswiriyu.

Mkulu oona za mbewu za gulu la chinangwa ndi mbatata kunthambiyo, Miswell Chitete, adati matendawa ndi ofunika kuwapewa chifukwa kupanda kutero, mlimi akhonza kupeza zokolola zochepa kwambiri.

“Alimi akuyenera kupewa matenda a chinangwa chifukwa ena mwa matendawa, mwachitsanzo khate, limatha kupangitsa chinangwa kuti chisabereke n’komwe kotero mlimi akhonza kungotaya mphamvu zake pachabe,” adatero mkuluyo.

Mphatso Jalasi, yemwe amachita bizinesi yolima ndi kugulitsa mbewu ya chinangwa m’boma la Zomba wati matendawa akupangitsa kuti mbewu ya chinangwa ikhale yoperewera. Iye adati kuperewera kwa mbewuyi ndi komwe kunamupangitsa kuti ayambe kulima ndi kugulitsa mbewu ya chinangwa.

Iye adati akuvutika kuti achulukitse mbewu ya chinangwa yopirira ku matendawa chifukwa siichita bwino kuchigawo cha kummwera.

“Ngakhale pali mbewu yopirira ku matendawa, mbewuyi ndiyosankha madera komanso ndi yowawa kotero pakufunika mbewu yosawawa komanso yosasankha Madera,” adatero Jalasi.

Chinangwa ndi imodzi mwa mbewu zomwe boma la Malawi lakhala likulimbikitsa alimi kuti azilima ngati njira imodzi yothana ndi mavuto a kusintha kwa nyengo komwe kwapangitsa kuti chakudya chizikhala choperewera mziko muno . Ngakhale izi zili chomwechi, nduna ya za malimidwe inayankhulapo mmbuyomu kuti matenda monga a khate komanso a kuola akuchepetsa zokola za mbewuyi mziko muno. Ichi ndi chifukwa chake akatswiri a za sayansi ali kalikiliki kufufuza njira yothana ndi matendawa. n

Related Articles

Back to top button
Translate »