Achita zionetsero za kuthimathima kwa magetsi

Anthu okhudzidwa a mu mzinda wa Lilongwe adachita ziwonetsero zosonyeza kukwiya kwawo ndi kuthimathima kwa magetsi m’dziko muno.

Cholinga cha ziwonetserozo chidali kukakamiza kampani yogulitsa magetsi Escom kuti ifotokoze, komanso kuthana ndi vuto la magetsi.

Vuto la magetsi lafika posauzana moti anthu ena akukhala tsiku lathunthu opanda magetsi.

Anthuwo, omwe adatsogoleredwa ndi mkulu wodziwika bwino pa nkhani yomenyera ufulu wa anthu Billy Mayaya, adakapereka chikalata kwa mkulu wa Escom wa m’chigawo chapakati McVitty Chiphwanya.

Anthuwo adanyamula zikwangwani zodzudzula mtsogoleri wa dziko lino, Peter Mutharika, kuti walephera kuthana ndi vuto la magetsi.

Padakali pano mkulu wa kampani yopanga magetsi ya Egenco, William Liabunya, wati boma lagula ma generator kuchokera ku India omwe achepetse vuto la kuthimathima kwa magetsi m’dziko muno.

Ma generator’wo aikidwa ku Blantyre, Mulanje, Mangochi ndi ku Mzuzu ndipo akuyembekezereka kuyamba kufika m’dziko muno kuyambira sabata ya mawa.

Share This Post