Chichewa

‘Adali kasitomala wa mchemwali wanga’

 

Mchemwali asamangokhala wokuphikira nsima kapena kukuthandiza kuchapa zikavuta, nthawi zina azikhalaso njira yokulondolera njira ya komwe kuli mbali ya nthiti yako.

Umu ndimo zidakhalira pakati pa Daniel Gunya, wa m’mudzi mwa Bubua, T/A Makwangwala m’boma la Ntcheu, ndi Beatrice Kamwendo, wochokera kwa Mchela, T/A Mlumbe, m’boma la Zomba.

Daniel akuti Beatrice amabwerabwera kumalo odyera a mlongo wake kudzagula zakudya ndipo awiriwo adayamba chinzake koma nthawi yonseyi akuti Daniel amangomezera malovu, osamasuka.

Daniel ndi Beatrice patsiku lomwe adachititsa chinkhoswe. Ukwati wawo udzamangidwa pa 29 October
Daniel ndi Beatrice patsiku lomwe adachititsa chinkhoswe. Ukwati wawo udzamangidwa pa 29 October

Iye akuti izi zidakhala zikuchitika kwa nthawi yaitali mpaka tsiku lina adatenga nambala ya lamya ya foni ya namwaliyo kwa mlongo wakeyo n’kumuimbira ndipo umu ndimo adayambira kucheza.

“Tidacheza ndithu kwa miyezi ingapo ngati munthu ndi mnzake mpaka m’chaka cha 2011 pomwe ndidamutengera kumalo osungirako mbiri (Museum) komwe ndidamuuza zakukhosi kwanga ndipo ndidalumphalumpha mumtima atandivomera,” adatero Daniel.

Iye akuti akaona Beatrice, amaona mnzake weniweni wokhala naye mpaka muyaya. Akuti amadzadza ndi chimwemwe komanso amapeza chilimbikitso cha mtundu uliwonse.

Beatrice akuti iye adali ndi malingaliro kuti Daniel adali naye nkhani chifukwa nthawi zonse akakumana kokagula chakudyako, Daniel amaonetsa nsangala yachilendo yosonyeza kuti waona chachikulu.

Iye akuti adaona mwamuna wachilungamo, wachikondi ndinso wodzichepetsa ndi wolimbika pochita zinthu ndipo izi zidamutenga mtima mpaka sadakaike konse kuti Mulungu ndiye adamutuma kuti azipita kumaloko.

Awiriwa adapanga chinkhoswe chawo pa 3 March chaka chino ku Nancholi ndipo pano adakonza kale tsiku la ukwati lomwe ndi pa 29 October cjaka chino pabwalo la zamasewero la College of Medicine mumzinda wa Blantyre.

Chosangalatsa nchakuti awiri onsewa amagwira ntchito zachipatala. Daniel amagwira ntchito pachipatala cha Neno ngati namwino pomwe Beatrice amagwira ntchito kuchipatala cha Beit Cure International ku Blantyre.n

Related Articles

Back to top button