Nkhani

Adutse ndani mu Standard Bank?

Listen to this article

Ndime ya kotafainolo mu Standard Bank Cup yafika podetsa nkhawa pamene matimu anayi akuyenera kutsanzikana ndi chikhochi sabata ino.

Pamene timalemba nkhaniyi dzulo n’kuti matimu a Civo ndi Dedza Young Soccer akuswana pa Civo Stadium. Dedza itatulutsa Kamuzu Barracks kudzera m’mapenote ulendo wapitawo, dzulo imayenera kuona ngati ulendo ukhale wopitirira kapena kuthera panjira.Wanderers_civo

Lero ndiye ulipo wankhodzo za pusi pa Kamuzu Stadium pamene Red Lions ithambitsane ndi Be Forward Wanderers.

Wanderers idatulutsa Mafco kudzeranso m’mapenote. Lero kodi Wanderers ichita zakupsa? Anthu ambiri ali ndi chikaiko malinga ndi kugonja motsatizana kwa Wanderers muligi ya TNM, koma kochi Elijah Kananji akuti awa ndi masewero osiyana ndipo akuona timu yake ikuphulapo kanthu lero.

“Anyamata akungofunika kuwalimbitsa mtima, koma ndilibe chikaiko malinga ndi momwe akumenyera kuti masewero ndi Red Lions titha kusangalala,” adatero Kananji.

Nayo Red Lions ikukumana ndi Wanderers itakumana ndi masautso pamene adagonja ndi Big Bullets 4-2 m’ligi. Koma Collings Nkuna akuti akubwera pa Kamuzu kuchokera ku Zomba ndi cholinga chofuna kupambana.

“Ija idali ligi, apa tikukamba za chikho. Tikuyembekeza kuti tichita bwino m’masewero amenewa,” adatero Nkuna.

Mpira wina lero ali pakati pa Silver Strikers ndi Blue Eagles pa Silver Stadium. Matimu onsewa zawayendera kumathero a sabata imeneyi muligi, Silver itapuntha Dedza 2-1 pamene Eagles idawalira Civo 4-1.

Silver, kukhala timu yomwe ikusunga chikhochi, sidagonjepo m’ligi chibwerereni Young Chimodzi ngati kochi.

Mawa ndiye kukhale fumbi ku Civo pamene Moyale Barracks ikhale ikusambitsana ndi Bullets. Bullets ikungochoka kosemphana ndi chikho cha Carlsberg chomwe idachisiya m’manja mwa Wanderers.

Related Articles

Back to top button