Adzipha atalephera kukachita ukachenjede

August 11, 2013 • Nkhani • Written by :

Makolo ndi abale a Jonathan Mayele wa zaka 20 ku Area 50 ku Lilongwe ali pa chisoni mbale wawoyu atadzipha pobwira simenti dzina lake litasowa pa mndandanda wa achinyamata ndi asungwana omwe asankhidwa kupita ku sukulu za ukachenjede.

Sabata ikuthayi boma lidaulutsa maina 1 909 a anthu amene asankhidwa kukachita maphunziro a ukachenjede koma Mayele yemwe akuti adakhoza mayeso a Folomu 4 ndi mapointi 10 kusukulu ya secondale ya Chaminade ku Karonga sadapezeke pa osankhidwawo.

Mchimwene wake Ganizani yemwe amalipira sukulu yake wati adapezeka atafa m’chinyumba chomwe chosamaliza mimba yake itafufuma.

Ganizani wati atapita naye ku chipatala madokotala adawauza kuti mnyamatayo adamwalira chifukwa chokanika kupuma chifukwa m’mimba mwake mudali simenti yomwe akuganiza kuti adakanda ndi kumwa.

“Mmene zotsatira za mayeso a ku yunivesite zimatuluka adali ku Zomba kwa amayi aang’ono koma tsiku lotsatiralo adabwerera. Amaoneka kuti adalibe mtendere koma tidayesetsa kumukhazikitsa mtima pansi. Tonse sitimayembekezera kuti angamusiye koma kudziphako walakwitsa kwambiri,” adatero iye.

Mneneri wa polisi ku Lilongwe Ramzy Mushani wati ngoziyo ndiyomvetsa chisoni koma wadzudzula mchitidwe wodzipha chifukwa chokhumudwa.

“Timadalira achinyamata kuti adzatilandire ntchito mtsogolo ndiye zikamakhala chonchi timamva chisoni chachikulu. Imfa yotere imapweteka makolo chifukwa amakhala ataononga ndalama zambiri. Achinyamata atamaganizira makolo ndi tsogolo la dziko zikhoza kuthandiza kwambiri,” watero Ganizani.

All views expressed in the comments of users of www.mwnation.com are independent. They are not a reflection of the views of Nation Publications Limited (NPL) nor are they endorsed by NPL. This is a forum provided by NPL to make good on it's corporate slogan of Making freedom of expression a reality.

Comments are closed.

« »