Nkhani

Afuna kudzikhweza nsanje itakula

Listen to this article

Apolisi ya Mponela ku Dowa amanga mayi wa zaka 24 Ketrina Paulo pomuganizira kuti amafuna kudzikhweza ponyansidwa ndi mwamuna wake yemwe adafuna kudya ndalama za utenanti ndi mkazi amene adalekana naye.

Mneneri wapolisiyo, Kondwani Kandiado, watsimikiza izi ponena kuti adamanga mayiyo pamlandu wofuna kudzipha zomwe zimatsutsana ndi ndime 229 ya malamulo a dziko lino koma koma amutulutsa pa belo chifukwa ali ndi ana amapasa ofunika chisamaliro koma  akaonekera kukhothi posachedwa.

Wojambula wathu kuyerekeza momwe zidalili

“Tidamanga mayiyo titalandira uthenga kuchoka kuchipatala komwe amati akalandire thandizo mwamuna wake atamupulumutsa. Akuti nkhani zake n’zabanja ndiye tamupatsa belo uku tikufufuza kuti tikhale ndi umboni wodzapita nawo kukhothi,” adatero Kandiado.

Malinga ndi mmodzi mwa anthu a m’mudzi mwa Msakambewa, Emmanuel Mazaza, banja loyamba la Skalioti Dzakande wa zaka 34 lidatha zitamveka kuti bamboyo adali ndi chibwenzi ndipo amafuna kutenga chiwiri.

Iye adati ngakhale zidali choncho, bamboyo sadasunthike ndipo mkazi woyambayo, Angela Kefa yemwe ali naye ana atatu atapita kwawo, iye adakatenga mkazi wachiwiriyo n’kulowana naye.

Dzinja lapitalo, bamboyo adakafuna ntchito ya utenanti ndipo adayipeza paesiteti ina yapafupi ndi kwawoko kenako adatenga mkazi wakeyo n’kupita naye kuntchitoko.

Monga mwa ndondomeko ya ntchito ya utenanti, banjalo lidagwirizana ndi mwini esiteti ndalama zomwe adzalipatse ntchito ikadzatha ndipo pomwe msika wa fodya uli mkati, bwanayo adalipira antchito ake kuphatikizapo banjalo.

Banjalo litalandira chachikulu cha Dedza komwe akulandira chithandizo cha mankhwala.

“Chomwe chidachitika n’choti mayiyo adapita kwa mnzake kukacheza ndipo pochoka kumeneko adazindikira kuti macheso palibe pakhomopo. Mayiyu adapita kunyumba yoyandikana nayo komwe adakabwereka machesowo kuti ayatsire moto.

“Nthawi yomwe adali kunyumba inayo kukabwereka macheso, mwamuna wakeyo adamutsatira kunyumba inayo kukamuuza kuti apite kunyumba kuti akakambirane nkhani ina,” adatero Manda.

Iye adati mayiyo adabwerera kunyumbako koma atangofika, bamboyo adatenga mpeni wakuthwa ndi kucheka nawo pakhosi pamkazi wakeyo ndipo zitatero bamboyo adathawa.

“Chifukwa chomwe adapangira izi sichikudziwa ndipo panopa kafukufuku wathu alimkati kuti tigwire bambo ameneyu ndipo tikamugwira akayankha mulandu ovulaza munthu,”  adafotokoza Manda. n

Related Articles

Back to top button
Translate »