Chichewa

Aganyu okhala ndi ziphaso

Listen to this article

Mwa zina zidabweretsa mawu woti tawuni ya Limbe imalira ochenjera, ndi kuberedwa kwa katundu ndi munthu yemwe udamukhulupirira kuti akunyamulire, wa ganyu. Tsopano padepoti ya Fumbi pali dongosolo lowumbanso chikhulupiriro chomwe chidagumuka pakati pa aganyu ndi mabwana komanso madona. TEMWA MHONE adakumana ndi Kassimu Sitande, mkulu wa anyamatawa, ndipo adacheza motere:

Sitande (Wachitatu kuchokera kumanja) ndi ena mwa aganyu

Akutanthauza chani anyamatawa ponena kuti ndi ovomerezeka?

Nkhani ndi ya chiphaso. Ichi ndi chilolezo chawo kuchita ganyu padepoti ya Fumbi ino. Komanso mabwana ndi madona asadere nkhawa kuti katundu wawo asowetsedwa.

Ganyu mpaka ziphaso?

Tilipo anthu 34 ndiye umboni wogwirika umafunika osati kungoyankhula kuti ndi waganyu. Zongodziwana ndi zimene zatiyika m’mavuto kwambiri zaka zapitazo. Kwina kulibe dongosololi, koma ntchito ndi unzika wa pano zimafuna chiphaso ndithu.

Fotokozani zifukwa zokhazikitsira ziphaso pakati panu?

Anthu akhulupirire kuti si ife okuba. Uku ndi kukhwimitsa chitetezo cha mabwana ndi madona komanso waganyu. Tikufuna kubwezeretsa chikhulupiriro mwa anthu kuti ife [aganyu] ndi wothandiza mu Limbe muno kunyamula katundu wawo. Kumbukirani kuti vakabu yakhala ikutivuta ndi kulepheretsa kupeza ndalama zochuluka. Apolisi ankatimanga pamlanduwu womwe timayenera kulipa ndalama zambiri, koma anthu sakutinyamulitsanso katundu. Iyinso ndi njira yoti anthu azidziwa wanyamula katundu ndi cholinga choti akathawa apezeke mosavuta. Bwana atenge chiphaso ndipo amubwezere wa ganyu akafika komwe amapita ndi kumulipira. Tikubweretsa dongosolo.

Koma mkalabongo umakuchotsani ulemu…

Iyayi. Zimenezo ndi zakale zomwe zatsala ndi aganyu ena osati ife. Pofika popanga ziphaso ndife ana odziwa dongosolo. Loweruka 2 koloko masana timakhala ndi maphunziro mmene tingalemekezere mwini katundu. Ngakhale amwe mkalabongo, amadziwa kasitomala ndi ofuna ulemu kuti apeze yomwera mawa komanso chakudya cha kunyumba. Mabwana ndi madona akanyamulitsa katundu adziwe dzina la mnyamata. Izi zimapezeka pachiphasochi ndipo akachitidwa chipongwe akuyenera kubwera kuti athandizidwe.

Zidatani kuti mupange gululi?

Kusiyanitsa akuba ndi aganyu. Lidalinso khumbo lomathandizana muzilinganizo zina komanso mavuto. Mukudziwa kuti maliro amafuna ndalama zambiri ndiye tidaganiza zomatengera wodwala kumudzi kwawo kuti zikavuta abale apepukidwe komanso kuzondana wina akadwala. Nthawi ya vakabu ija timasonkherana ndalama yokawombola mnzathu akamangidwa kupolisi.

Ndi chiyani chomuyenereza munthu kukhala waganyu?

Chidwi chonyamula basi. Koma abwere kuofesi kuti amve malamulo ndipo akagwirizana nawo ndi mfulu pano.

Chifukwa chiyani anyamatawa akusiya ziphaso poweruka?

Iyi ndi njira imodzi yoteteza chiphaso chifukwa angataye kapena kuwabera kumowa. Anthu akhonza kukaba kwina ndi kuchita chipongwe pochitaya [chiphaso] ndi kupachika mnyamata wathu. Ntchito timayamba 6 koloko m’mawa yomwe timagawira ziphasozi ndipo kuweruka 5 koloko madzulo. Paja malo ano [mlatho pamtsinje wa Limbe] athu amachitidwanso chipongwe ndiye timaweruka [5 koloko] kuti zisatikhudze za chifwambazo.

Ofesi yanu imachitanso chiyani?

Timagwira ntchito ndi mabungwe osiyanasiyana polimbikitsa anyamatawa kuyezetsa magazi komanso okwatira kumalera. Tili ndi dongosolo lopereka peshoni (K4 000) kwa waganyu yemwe adakula pa 15 mwezi uliwonse kuti asachite kusowa ya sopo. Ndalamazi ndi zomwe mamembala timapereka pa sabata. Pakadalipano, tikudikira yankho kupolisi ya Limbe pa pempho lathu logwira nawo ntchito pokhwimitsa chitetezo.

Mavuto omwe mumakumana nawo ndi ati?

Kukanika kwa anthu kutipatsa ntchito chifukwa cha zikhomo adakumana nazo kale. Ena amatinyozanso kuiwala kuti tonse sitingakhale mabwana. Koma sitizitengera podziwa kuti Mulungu amatithokoza kaamba ka madongosolo obweretsa bata mu Limbe.

Mawu kwa mabwana ndi madona ofika mu Limbe?

Mtendere kwa ogula zinthu mu Limbe sungapose kunyamulitsa wa ganyu ali ndi chiphaso. Ife si akuba. Kugwiritsa ntchito opanda chiphaso ndi kufuna ndipo zikavuta sizitikhudza komanso osayerekeza kubwera chifukwa mwaziputa dala. Wachiphaso sangabe, koma akapulikira malangizo athu katundu wawo azapezeka ndithu. n

Related Articles

Back to top button