Nkhani

Agwira ‘onyoza’ mtsogoleri wa dziko lino

Amayi awiri ati apolisi adawamanga sabata ikuthayi powaganizira kuti adanyoza mtsogoleri wadziko lino, Joyce Banda ndi chipani chake cha People’s Party (PP) ati atakana kulandira chovala chamakaka achipanichi kuti avinire mtsogoleriyu.

Amayiwa ati adakananso kulowa m’gulu la amayi anzawo omwe amavinira mtsogoleriyu pomwe adakayendera dera lawo.

Oganiziridwawa, Eliza Kusheni wazaka 26 ndi Dorothy Ng’onga wazaka 24 adatulutsidwa pabelo la bwalo lamilandu la Mwanza Magistrate Lolemba atakhala masiku asanu m’chitokolosi cha apolisi.

Wapolisi wamkulu ku Mwanza, Ellobiam Banda, adatsimikizira zakunjatidwa kwa awiriwo koma iye adati amayiwo sadamangidwe pochitira mtudzu mtsogoleri wadziko lino monga akunenera.

Iye adati kumangidwa kwa awiriwo kudadza malinga ndi kusagwirizana pakati pa iwo ndi amayi am’deralo.

“Amayi awiriwa agamulidwa pogwiritsa ntchito mawu onyoza.

Zikuganiziridwa kuti amayi awiriwa adanyoza mayi wina, Martha Mazinzi potsatira nsanje yomwe idakula,” adatero wapolisiyu.

Iye adati atangonjata amayiwo Lachinayi, oganiziradwawo adatulutsidwa pabelo Lolemba chifukwa apolisiwo adali otangwanidwa ndi mtsogoleri wa dziko lino pomwe amakayendera kumeneko.

Zotolera za apolisi zikutsutsana ndi zimene oganiziridwawo komanso mkhalakale wachipani cha DPP, Bright Kachingwe kumeneko akunena.

Ng’onga wati iye ndi mayi mnzakeyo adazizwa ndikumangidwa kwawo chifukwa patsikulo sadachitire mtudzu aliyense.

“Patsikulo timachokera kundende ya Mwanza pomwe tidakumana ndi amayi 6, mmodzi mwa iwo adavala chovala cha makaka achipani cha PP, ndipo ndidathirira ndemanga kuti chovalacho chidali chabwino,” adatero mayiyo.

Ng’onga adati atazindikira kuti zinthu zidayamba kutentha, iye ndi mnzake adachoka pamalopo pomwe adabisala m’golosale yomwe awiriwo amagwira ntchito.

Iye adati apolisi adabwera pamalopo kudzawanjata popanda zifukwa zokwanira.

Awiriwo adatulutsidwa pabelo posapereka chikole chilichonse. Bwalo lidalamula kuti awiriwo adzikawonekera kupolisi Lolemba lililonse.

Kachingwe adati chipani ndichokhudzidwa ndi kunjatindwa kwa awiriwo.

Related Articles

Back to top button