Chichewa

Akhalenso ndi moyo wautali

Listen to this article

 

Tsiku limenelo ndidakwiya zedi pa Wenela. Mkwiyo wanga udali waukulu zedi moti ndidafuna kuphulika. Inde, udali mkwiyo waukulu zedi moti kuchita chibwana nzimbe ndithu ikadamera pamsana!

M’minibasi imene ndinkaitanira nthawi imeneyo munkalira nyimbo ya King Yellowman, inde, mmodzi mwa oimba chamba cha dancehall kuchokera ku Jamaica. Mutu wa nyimboyo ndi Zungguzungguguzungguzeng. Amene sakuidziwa nyimbo imeneyi ngoyenera kudzidabwa chifukwa inetu ngakhale ndili kwathu kwa Kanduku, mawu ake ndinkawadziwa bwino:

art

Zungguzungguguzungguzeng

Zungguzungguguzungguzeng

Seh if yuh have a paper, yuh must have a pen

And if yuh have a start, yuh must have a end

Seh five plus five, it equal to ten

And if yuh have goat, yuh put dem in a pen

And if yuh have a rooster, yuh must have a hen, now:

Chidandikwiyitsa kwambiri chidali chakuti m’minibasimo mudatsika munthu wachialubino. Mzibambo adabopha ulusi mochititsa kaso. Atatsika munthuyo, anthu adayamba kuliza malikhweru. Ena adali kukuwa: “Mamiliyoni awo!!!”

Mawu amenewa ndiwo adandikwiyitsa zedi. Ndidagwira mmodzi mwa anthu amakuwawo. Ndidamulawitsa makofi.

“Kupusa! Amene mukukuwa zopusazi ndinu oipa, chimodzimodzi amene amapha maalubino ati kuti akachite zizimba. Kulemera kwake kuti? Ndipo chuma chake chodyedwa ndi njenjete chomwechi?” ndidafunsa mozaza.

Nditapita kumalo aja timakonda, ndidapeza akuvina nyimbo ya Kenneth Ning’ang’a ndi Geoffrey Zigoma. Koma kudali dansi yotha malo. Ndipo mawu anthetemya a Zigoma adanditenga mtima osakhala masewera.

Mayo mayo, mayo mayo ndathera pano!

Takondwera mwalowa m’banja aye….

Itatha nyimboyo, wapamalopo, Gervazzio, adatsegula wailesi kuti timvere nkhani.

“Mwina n’kumva kuti Moya Pete wanenapo chiyani za kubedwa, kuphedwa ndi kunyozedwa kwa maalubino,” adatero.

“Woweruza milandu wina walamula kuti munthu amene anaba munthu wachialubino wina akaseweze kundende zaka ziwiri,” adali kutero wowerenga nkhani.

Abiti Patuma adakwiya. Mtima wake umachita kumveka kugunda ngati uphulika!

“Zaka ziwiri basi? Munthuyo amafuna akagulitse munthu wachialubinoyo kuti achotse ziwalo zina ati zizimba ndiye kungomupatsa zaka ziwiri kundende? Munthu wakuba ng’ombe akupatsidwa zaka 7 koma wakuba munthu mnzake kungopatsidwa zaka ziwiri basi?” adazaza.

Nanenso mkwiyo udachititsa mwazi wanga kuthamanga.

“Zilango amati zizichititsa ena kuti asayerekeze kupalamula. Chilango ngati ichi chingaopseze ena? Enatu akufukula mitembo ya maalubino ati zizimba. Ayi ndithu, ufiti wotere wafika povuta,” ndidatero.

Mkwiyo wandizinga. Mtima wanga ukupweteka. Ndikumva kutentha ngati munthu wodya nsima yamoto, ndiwo zake khwanya wothiridwa tsabola wakambuzi wochuluka komanso atakhala padzuwa la 12 koloko masana.

M’mutu mwanga mudayamba kuyenda nyimbo ya Salif Keita. Ngati mu Africa muli anthu odziwa kuimba, Salif Keita ndi mmodzi mwa iwo. Ngakhale ndi wachialubino, Salif ali ndi luso ndipo amadziwika padziko lonse lapansi chifukwa cha nyimbo zake zogwira mtima. Ndimukumbuka bwino chifukwa tsiku lomwe adabwera ku Malawi ndidanyamula zikwama ndi magitala ake kulowera ku French Cultural Centre.

Nyimbo yake idali ya Folon, imene adaimba ndi wotchuka winanso, Youssour N’dor.

“Koma abale nkhanza izi ziyenera kutha. Momwe ndikuonera mchitidwe wonyansawu udayamba kalekale. Ndikumbuka kalekale tinkauzidwa kuti ma alubino amangosowa, samwalira. Ndiye kuti nkhanzazi zidayamba kale. Anthu akuba anzawowa adayamba izi kalekale,” adatero Abiti Patuma.

Abale anzanga mkwiyo wanga ndi waukulu zedi. Nchifukwa chake lero sindinena konse za gwira bango upita ndi madzi. Nchifukwa chake ndikuti mtima wanga uli ndi amayi, abambo komanso ana onse achialubino amene akuchitiridwa nkhanza zotere ndi anthu adyera. Ndi pemphero langa pamene ndikujiya usiku ndi usana kuti anthu achialubino atetezedwe kunkhanzazi ndipo nawo akhale ndi moyo wautali. Ndani safuna kukhala ndi moyo? n

Related Articles

Back to top button
Translate »