Chichewa

Akhazikitsa tindege tothandiza zaumoyo

Listen to this article

 

Pali chiyembekezo chakuti mavuto omwe amakumana nawo ogwira ntchito m’zipatala za kumidzi ndi anthu okhala m’maderawo achepa ndi makina  a tindege otchedwa drone m’Chingerezi polumikizitsa maderawa ndi zipatala zikuluzikulu.

Unduna wa Zaumoyo, nthambi yoyendetsa za maulendo a pa ndenge ndi bungwe loyang’anira za umoyo wa ana la Unicef atsimikiza za ndondomekoyi yomwe ati yayamba kale kugwira ntchito m’madera ena.

Kamodzi mwa tindegeto

Mneneri wa bungwe la Unicef Doreen Matonga wati ogwira ntchito m’zipatala za kumidzi amakumana ndi mavuto adzaoneni popereka ndi kulandira thandizo la zaumoyo komanso pakakhala ngozi zodza mwadzidzidzi Madera ena amavuta kufikako.

Iye adati mavuto odziwika kwambiri ndi nkhani ya mayendedwe pokatenga mankhwala kuchipatala chachikulu kapena pokayezetsa magazi ndi makhololo komanso polandira zotsatira za zoyesazo.

“Tidapeza kuti pali zipatala zina zomwe ogwira ntchito amayenera kupalasa njinga mtunda pafupifupi makilomita 70 kuti akatenge mankhwala kuchipatala chapaboma ndi kubwereranso mtunda onga omwewo.

“Kuwonjezera apo, pakakhala zofunika kuyeza monga malungo kapena makhololo, pamatenga nthawi kuti zikafike ku chipatala chomwe amayeza komanso kuti zotsatira zake zifike pomwe wodwalayo akungodikilira,” adatero Matonga.

Iye wati apa azikgwiritsa ntchito tindegeto, timenenso tizithandiza kujambula zithunzi za Madera amene kwagwa ngozi komanso kupititsa patsogolo ntchito za Internet.

Mneneri wa unduna wa zaumoyo Adrian Chikumbe wati ndondomekoyi idayamba mmwezi wa February m’madera ochepa ndipo idakhazikitsidwa mwezi watha kuti iwunikidwe ngati ndiyothandizadi.

“Ikangogwira, mavuto ambiri atha chifukwa nzoonadi kuti anthu a mmadera a kumidzi amakumana ndi mavuto kuti alandire thandizo moyenera,” adatero Chikumbe.

Woyang’anira za maulendo a ndenge ku unduna wa za mtengatenga Hastings Jailosi wati  ndondomeko yonse yaunikidwa kale bwinobwino ndipo sipazikhala kusokonezana pakati pa tindengeti ndi ndenge zikuluzikulu zonyamula anthu ndi katundu.

Iye wati tindegeti tikhala m’masayizi osiyanasiyana ndipo tizinyamula katundu wa milingo yosiyanasiyana.

“Tina tikhoza kunyamula katundu wolemera makilogalamu 25 ndipo tina n’tocheperako,” adatero Jailosi.

Iye wapempha anthu kuti asamadabwe akawona tidengeti tikuwuluka mmadera awo poganiza kuti ndi ufiti kapena tauchigawenga koma kuti ntowathandiza pochepetsa mavuto ena pa nkhani za umoyo mmadera awo. n

 

Related Articles

Back to top button