Nkhani

Akhoti anyanyala ntchito

Listen to this article

Mavenda 40 omwe adamangidwa mu mzinda wa Lilongwe sabata yathayi ali m’gulu la anthu zikwizikwi za anthu amene akhudzidwa ndi kunyanyala ntchito kwa anthu ogwira ntchito m’mabwalo amilandu m’dziko muno komwe kunayambika Lolemba lapitali.

Chifukwa chakusayenda kwa zinthu m’mabwalo amilanduwa iwowa alephera kupeza belo kapena chithandizo china chilichonse ndipo afinyikabe mpaka kunyanyala ntchitoku kutatha.

Onyanyala ntchitowa ati akuchita izi pofuna kukakamiza boma kuti liyambe kupereka malipiro omwe adagwirizana m’chaka cha 2006.

Apa akatswiri pa ndale, amabungwe komanso anthu otumikiridwa ndi mabwalowa ati boma likuyenera kulongosola izi madzi asadafike m’khosi.

Kuyambira Lolemba mabwalo amilandu adali otseka, ndipo pofika Lachitatu pomwe timasindikiza Tamvani, mabwalowo adali asadawatsegule.

Malinga ndi mkulu wa bungwe loona zaufulu wa anthu la Malawi Watch Billy Banda wati kunyanyala ntchitoko kwasonyeza kuti boma silikulabadira miyoyo ya anthu.

Banda wati ngati kunyanyalaku kungapitirire, Amalawi ambiri avutika chifukwa pali ena omwe sakuyenera kukhala kundende koma ali kumeneko chifukwa cha kunyanyala ntchitoku.

Mavenda 40 omwe adamangidwa ku Lilongwe pazipolowe amayenera kukaonekera kubwalo lamilandu Lolemba koma sizidatheke chifukwa cha sitalakayo.

Mneneri wa polisi m’chigawo chapakati, John Namalenga, Lachiwiri adavomereza kuti anthuwa adalephera kukaonekera kubwalo lamilandu chifukwa choti kumabwaloko kudali kotseka.

Iye adati kunyanyalaku kukapitirira ndiye kuti zitokosi zam’dziko muno zikhala zodzadza.

“Ngati anthu achuluka m’chitolokosi timakawasunga ku polisi za Kawale ndi Lingadzi. Koma ngati kunyanyalaku kungapitirire tisowa pogwira.

‘Kudzadzaku kungachitike ngati titamanga anthu ambiri pakamodzi chifukwa zimatheka kumanga anthu oposa 100 patsiku,” adatero Namalenga.

Mphunzitsi wa zandale kusukulu ya ukachenjede ya Chancellor College, Joseph Chunga, wati uku ndikupha ufulu wachibadwidwe makamaka kwa anthu omwe ali m’manja mwa apolisi chifukwa amayenera kukaonekera kubwalo lamilandu kuti akapatsidwe belo kapena kuti akadziwike ngati ndi wolakwa pa mlandu omwe amangidwira.

“Monga mwa malamulo, pamayenera pasadutse maola 48 omangidwa asadakaonekere kubwalo lamilandu. Ngati izi sizidatsatidwe, ndiye kuti ufulu wako waphwanyidwa.”

Iye adati kunyanyalako kukapitirira pali chiopsezo kuti boma lingatengerepo mwayi chifukwa lidziwa kuti munthu akamangidwa sakaonekera kubwalo la milandu.

“Izi zikutanthauza kuti ulamuliro wotsatira malamulo watha,” adatero Chunga.

Ndipo Osman Chimenya wa ku Kanjedza mumzinda wa Blantyre adavomerezana ndi Chunga ndipo adati boma likuyenera kukwaniritsa mgwirizano wake ndi ogwira ntchitowa.

Erick Gomani wa ku Malewule kwa T/A Kapeni m’boma la Blantyre adaikira mang’ombe, ndi kuti anthuwa adalonjezedwa kuti apatsidwa malipiro atsopano kotero boma likuyenera kukwaniritsa.

Mneneri wa gulu lomwe likunyanyalali yemwenso ndi kalaliki wamkulu ku High Court mumzinda wa Blantyre, Austin Kamanga wati sasintha ganizo lonyanyala ntchito pokhapokha boma litayamba kupereka ndalama zomwe zidavomerezedwa ndi Nyumba ya Malamulo m’chaka cha 2006.

Iye adati malipiro a anthu omwe amagwira ntchito zina kumabwalo amilandu amavomerezedwa ndi nduna ya zachuma zomwe akuti zidachitika mu 2006 koma boma silidafune kukwaniritsa.

“Kuyambira 1997, malamulo akagwiridwe ka ntchito a ogwira ntchito kumabwalo amilandu amaunikidwa pakatha zaka zitatu, ndipo akaonedwa amatumizidwa kunyumba ya malamulo kuti aphungu akaunikire ndikuvomereza,” adatero Kamanga.

Mu 2006, Nyumba ya Malamulo itavomereza komanso nduna ya zachuma itavomereza, anthuwa akuti sadalandire malipiro atsopanowo ndipo kukokanakokana kudayambika.

Kamanga adaonjeza kuti: “M’chaka cha 2009, boma lidangolengeza kuti litionjezera malipiro ndi K15 pa K100 iliyonse koma sitikumvetsa kuti ndalama imeneyi imachokera pati?

“Tikufuna tiyambe kulandira ndalama zathu, apo ayi sitibwerera kuntchito,” adalumbira Kamanga.

Nduna ya zachuma, Ken Lipenga, samayankha lamya yake ya m’manja pomwe Tamvani imafuna kulankhula naye.

Koma iye adauza atolankhani Lachiwiri m’sabatayi kuti unduna wake ukukambirana ndi okhudzidwa kuti ayankhe mavuto a anthuwa.

Iye adati alankhulapo pa nkhaniyo akangomaliza kukambirana ndi mbali zokhudzidwa pa nkhaniyo.

Related Articles

Back to top button