Nkhani

Akufuna wogwirizira ufumu achoke, apepese

Mafumu m’dziko muno agwirizana ndi ganizo la mtsogoleri wa dziko lino Joyce Banda kuti magulupu ndi nyakwawa asiye kulandirira ndalama kubanki.

Banda adalankhula izi sabata yatha pasukulu ya Nsumwa m’boma la Salima poyankha pempho la mfumu Ndindi kuti mafumu akuvutika pokalandirira ndalama kubanki.

Polandira Banda, Ndindi adati ndondomeko yomwe idayambitsidwa m’boma la chipani cha DPP kuti iwo adzikalandilira mswahala kubanki yazunza mafumuwa ponena kuti ndalamayo imathera ulendo.

Apa Banda adati nyakwawa ndi magulupu asamakalandirirenso ndalama kubanki ponena kuti ndondomeko yapoyamba ibwezeretsedwa.

Apa mafumuwa ati nkhaniyi iwathandiza chifukwa ndalamayo samaiwona ubwino wake malinga n’kuti komwe kuli mabanki ndi komwe amakhala ndi mtunda wautali.

Nyakwawa Kapoti ya kwa T/A Zilakoma m’boma la Nkhata Bay yati kuchokera m’mudzimo kukafika kuboma komwe kuli mabanki ndi mtunda omwe amalipira K2 000 kupita ndi kubwera.

Mfumuyi yauza Tamvani kuti penanso akapita ndalamazo amakapeza zisadalowe.

“Ndimalandira K2 500 ndipo ndimaononga K2 000 kusonyeza kuti malipiro anga ndi K500. Apa tiyamike kuti tizilandira kumudzi kuno,” idatero mfumuyo.

Gulupu Chisinkha ya m’boma la Mulanje kwa T/A Mabuka yati mfundo ya boma ili bwino bolani ndalamazo adziwapatsadi.

“Ndondomeko yapoyambayonso idali ndi mavuto ake pomwe pena malipiro sitimalandira. Ganizoli n’labwino bola tizilandira,” adatero Chisinkha.

Mtsogoleri wakale wa dziko lino, Bingu wa Mutharika ndiye adalamula kuti aliyense wogwira ntchito m’boma kuphatikiza mafumu adzikalandira malipiro awo kubanki.

Related Articles

Back to top button