Nkhani

Akukambirana zolola ana a chi Rasta m’sukulu

Listen to this article

Unduna wa za maphunziro wati ukukambirana ndi ma Rasta komanso unduna wa za malamulo pa za ana 26 amene ma Rasta adapempha kuti aziloledwa kuphunzira m’sukulu za boma ali ndi tsitsi la mizere—madiredi.

Anawa, amene padakali pano sakupita kusukulu, akuimira ana ena onse a ma Rasta amene amaletsedwa kusunga tsitsi lopotana m’sukulu za boma za m’dziko muno.

Mwanamanga: Tinkakambirana ndi Bingu

Kalata yomwe unduna wa za malamulo udalembera unduna wa za maphunziro pa 27 January, 2017, idaunikira kuti undunawo ukuyenera kulandira mwana aliyense, kuphatikizapo ana amene akusunga tsitsi lopotana, malinga ndi chipembedzo chawo.

“Potengera ndi kulemekeza mphamvu ya malamulo a dziko lino, pa magawo 20, 25 ndi 33, ndi ufulu wa m’Malawi, aliyense kusasalidwa ndipo munthu aliyense ali ndi ufulu wolandira maphunziro komanso otsatira chipembedzo chomwe akufuna.

“Kotero, potengera kusintha lamulo lokhudza maonekedwe ndi za kavalidwe pakati pa ophunzira, lomwe limaletsa kusunga tsitsi pasukulu, mukuyenera kulola ana omwe ali ndi tsitsi lopotana potengera chipembedzo cha chi Rasta m’sukulu za boma,” idatero kalatayo.

Mneneri wa unduna wa za maphunziro Lindiwe Chide adati undunawu ukudziwa za kalata yochokera ku unduna wa za malamuloyo ndipo adati undunawo ukukambirana ndi mbali zonse zokhudzidwa pa momwe izi zingatsatidwire.

“Tikukambirana ndi mbali zosiyanasiyana zokhudzidwa za momwe tingayendetsere pulogalamuyi ndipo zikatheka mumva sizidzasowa,” adatero Chide.

Sukulu za boma za pulaimale ndi sekondale m’dziko muno zimathamangitsa ana omwe ali ndi tsitsi lopotana potsatira chipembedzo cha u Rasta ndipo nkhaniyi siyikondweretsa mpang’ono pomwe eni chipembedzochi.

Kwa zaka zoposa 20 tsopano, otsatira chipembedzochi akhala akumenyerera kuti unduna wa zamaphunziro usinthe maganizo n’kuyamba kulola anawa m’sukuluzi kuti nawonso azidyerera ufulu wawo wamaphunziro.

Mtsogoleri wachipembedzochi m’dziko muno m’gawo la Nyabinghi, Ras Mikah Chiserah wati zomwe zikuchitikazi zikutanthauza kuti dziko la Malawi silivomereza chipembedzo cha chi Rasta monga momwe malamulo amanenera.

“Apatu zikutanthauza kuti ife ma Rasta tikufera chipembedzo chonsecho malamulo amati munthu aliyense ali ndi ufulu otsata chipembedzo chomwe akufuna pambali pa ufulu wa maphunziro,” adatero Ras Chiserah.

Iye adati pomwe ufulu wa zipembedzo unkabwera kumayambiliro a ulamuliro wa zipani zambiri, iwo ankaona ngati kuponderezedwa kwa owutsatira kwatha koma akudabwa kuti boma likulephera kutsatira malamulo opanga lokha.

Kadaulo pa zamalamulo yemwenso ndi mphunzitsi ku sukulu ya ukachenjede ya Chancellor College ku thambi ya zamalamulo, Edge Kanyongolo adati ufulu uli ndi mlingo wake koma akaunika nkhani ya ma Rastayi, saonapo vuto.

“M’malamulo a dziko lino muli maufulu osiyanasiyana ndipo umodzi mwa maufuluwa n’kukondedwa mofanana. Chifukwa chokhacho chomwe ufulu ungapatsidwe mlingo, mpomwe ukuphwanya ufulu wa anthu ena ndipo sindikuona kukhala ndi tsitsi lopotana kukuphwanya ufulu wa munthu wina,” adatero Kanyongolo.

Malingana ndi mneneri wa Nyabinghi, Ras Fred Mwanamanga, kusunga tsitsi lopotana ndi umodzi mwa mizati ya chipembedzo cha chi Rasta ndipo kuti ngati Amalawi, otsatira chipembedzochi amayenera kuloledwa kupanga chilichonse chomwe otsatira zipembedzo zina amaloledwa kupanga.

Pomenyerera ufulu wa maphunziro omwe Mwanamanga adati otsatira chipembedzochi amamanidwa, ma Rasta adakumana ndi mtsogoleri wakale Bingu wa Mutharika yemwe adawalonjeza kuti zonse zikhala bwino.

Mwanamanga adati mwatsoka, zisadakhale bwino monga momwe amayembekezeramo, Mutharika adamwalira ndipo izi zidachititsa kuti ma Rastawa ayambirenso nkhondo yomenyerera ufulu wawo.

“Titangomva za imfa ya a Mutharika, tidasweka mitima chifukwa tidadziwa kuti ntchito ikadalipo. Mu 2013, tidayenda ndawala yokapereka kalata ya madandaulo kulikulu la dziko lino ku Lilongwe komwe tidayankhidwa kuti madandaulo athu apita kwa a Pulezidenti,” watero Mwanamanga.

Iye wati pakhala pakuchitika zokambirana pankhaniyi pakati pa ma Rasta, unduna wa zamaphunziro, unduna wa za malamulo ndi magulu a zamaufulu ndipo potsatira zokambiranazi, unduna wa za malamulo udalangiza unduna wa za maphunziro kuti uyambe kupereka mpata kwa ophunzira a chipembedzo cha chi Rasta. 

Related Articles

Back to top button
Translate »