Akupopa zimbudzi pochepetsa matenda

Ena zimbudzi zawo zikadzadza amagwetsa ndi kukumba china. Uku ndi kutha malo. Lero zinasintha chifukwa khonsolo ya Blantyre mogwirizana ndi Waste Advisers agwirizana zopopa zimbudzi zomwe zadzadza.

Iyitu ndi njira yomwe mbalizi zamvana pofuna kulimbikitsa ukhondo mumzinda wa Blantyre pamene matenda a kolera akugwetsa anthu moti kufika lero anthu 26 amwalira.

Kupatula izi, khonsoloyi ikuyenda khomo lililonse mumzinda wa Blantyre kuphunzitsa anthu zaukhondo ndipo nyumba 10 000 azifikira.

Amene akuwongolera ntchitoyi ku bungwe la Waste Advisers, Marcel Chisi, adati kupatula ntchitoyi, amanga zimbudzi 30 mwa zimbudzi 100 mumzindawu kuti ukhondo upite patsogolo.

“Tisamangonena kuti anthu asakodze paliponse koma tikuyenera kumanga zimbudzi kuti anthu azilowa m’menemo polipira kangachepe,” adatero Chisi.

“Tagwirizana ndi makampani amene akugwira ntchito yopopa komanso kumanga zimbudzi zamakono. Anthu akatipeza, tiwalumikizitsa kwa amene angawathandize.”

Chimpopa chimodzi chimapopa zinthu zochuluka malita 3 600 ndipo munthu alipira K30 000.

Komanso mtengo umasintha malinga ndi kutalika kwa malo amene akapopawo.

Wachiwiri woona nkhani za umoyo ku khonsolo ya Blantyre, Samden Seunda adati zonyansazo zikapopedwa azizipititsa ku Chirimba, Soche, Blantyre ndi ku Limbe komwe azikazithira mankhwala.

“Tili ndi chikonzero kuti zonyasazo tizizithira mankhwala ndipo kutsogolo kuno tizipangira nkhuni zomwe mutha kuphikira,” adatero Seunda.

 

Share This Post