Chichewa

‘Akwawo ankati Ichocho ndi choopsa’

 

Ntchito ndi maonekedwe a Yasin ‘Ichocho’ Suwedi, mmodzi mwa akatswiri pankhani yofufumitsa minyewa, ndizo zidali zolepheretsa kuti akwatire Fatima Assed Chipoka, namwali amene maso ake adamulozera.

Ichocho, amadziwika kwambiri ndi kunyamula zitsulo komanso kufufumitsa minyewa zomwe akwawo kwa Fatima samakondwera nazo kuti mwana wawo atengane ndi mwamuna wotere.

Koma danja la Mulungu likalemba lalemba, njira idapezeka kuti zomwe zidalembedwazo zikwaniritsidwe pamene awiriwa adakwatirana.

Banja la Ichocho lili ndi ana atatu tsopano
Banja la Ichocho lili ndi ana atatu tsopano

Kodi mkuluyu adakumana ndi zokhoma zotani? Ntchito idayamba mu 2008 pamene iye adali ndi lingaliro lokhala pabanja. Monga Msilamu, mkuluyu ankafunanso kachisilamu.

Mu April akuti adakumana ndi Fatima. Atangomuthira diso, thupi lake ngakhale lili la dzitho komabe lidazizira, nthumanzi idamenya nganga yake, akuti adadziwa kuti waona mngelo wake. Umo mudali mumsika wa Ndirande.

“Kodi ndi Msilamu? Nanga bwanji sadavale hijabu?” adadzifunsa Ichocho. “Ndidamufunsa dzina ndipo lidali la Chisilamu, aaaa!”

Thupi lidalefuka, nkhani zachikondi zidalenga ngati msozi m’thupi mwake. Nkhondo ya mawu idayambika.

Chifukwa cha maonekedwe ake ali oopsa, mbalume zonse zidaomba khoma chifukwa akwawo kwa Fatima adakana.

“Ngati ufuna chikakuphe chita zomwe ufunazo,” adatero Fatima kutsanzira momwe akwawo adanenera.

Tiatsikana tinanso tidamuuza Fatima kuti asalole. Koma chikondi chilibe maonekedwe, tsiku lidakwana kuti zolembedwa zikwaniritsidwe. “Ntchito yawo yonyamula zitsuloyi ndi yomwe aliyense amadana nayo.”

Kumapeto kwa 2009 adafewa mkamwa. “Anthu amati ndi wandewu koma sindimaona zimenezo, ndidalola ngakhale ena amandiletsabe. Pali chikondi palibe mantha,” adatero Fatima

July 2010, chinkhoswe chidatheka. Lero m’nyumbamo mwatuluka mphatso zitatu ndipo Fatima watsimikiza kuti Ichocho si munthu wandewu. Zomwe amaopa anthu zija sizichitikamo m’banja lawo.

Koma mu 2013 nkhondo m’nyumbamu idabadwa. Mkaziyu akuti amakanitsitsa kuti asamakachite nawo mpikisano wofufumitsa minyewa (body-building) chifukwa akamachita mpikisanowu amavala timakabudula tamkati tokha, zomwe sizigwirizana ndi Chisilamu.

“Ndidayesera kumupatsa zitsanzo kuti si tchimo ndipo pano zonse zili tayale,” adatero Ichocho, yemwe akuti amene amachita masewero ofufumitsa minyewa asamazunze akazi awo.

Mwana womaliza wa banjali ndi wamwamuna, Hamizar Ichocho Suwedi, amene ati ndiye atenge ntchito za Ichocho. n

Related Articles

Back to top button