Nkhani

Akwiya ndi bungwe la MEC

Listen to this article

Mpungwepungwe umene ukuchitika kubungwe loyendetsa zisankho la Malawi Electoral Commission (MEC) wakwiyitsa zipani zotsutsa komanso omenyera ufulu omwe apempha kuti zinthu zikonzedwe msanga kubungweli kuti ntchito yochititsa zisankho isaime chifukwa kutero n’kuphwanya ufulu wa anthu wosankha atsogoleri awo.

Mneneri wa chipani cha People’s Party (PP) Ken Msonda, komanso wa chipani cha UDF Ken Ndanga kudzanso mkulu womenyera ufulu wa anthu, Unandi Banda, apempha bungweli kuti likonze zinthu msanga kuti zipani zonse zikhale ndi chikhulupiriro pa bungweli.

Msonda: Sitikukondwa nazo zimezi
Msonda: Sitikukondwa nazo zimezi

Ndemanga za akuluakuluwa zikudza pamene kubungweli kwachitika zingapo monga kulephereka kwa zisankho zachibwereza m’madera asanu; kusokonekera kwa ndalama; kutumizidwa kutchuthi kwa akuluakulu ena a bungweli mokakamizidwa; komanso pamene bungweli likutha masiku opanda wapampando chimwalirireni mwadzidzidzi amene adali mtsogoleri Maxon Mbendera.

Msonda adati zomwe zikuchitika ku MEC zikuonetseratu kuti bungweli silikugwira ntchito mokomera zipani zotsutsa.

“Kutumiza ogwira ntchito ena kutchuthi ndi nkhani yabwino, chifukwa tikufuna tidziwe momwe ndalama [zoposa K15 miliyoni] zidasowera. Koma vuto lathu ndi kuimitsa zisankho [zapaderazi] kuti zisachitike.

“Ife sitikukondwa nazo, zikuonetseratu kuti bungweli likunjenjemera ndi boma. Ichi n’chipongwe kuti zisankho zapadera zisachitike. Tadandaula nazo,” adatero Msonda.

Iye adati kusachititsa zisankho zapaderazi ndi kuwaphwanyira ufulu anthu a maderawo chifukwa ntchito zachitukuko komanso zakumtima kwawo sizingapherezere kaamba kosowa wokatula nkhawa zawo ku Nyumba ya Malamulo kapena kukhonsolo.

Naye Ndanga adati chikuwadandaulitsa iwo si kuimitsidwa kokha kwa zisankho chachibwereza, koma kuti izi zingakhudze chisankho cha 2019.

“Ntchito yochititsa chisankho simangochitika tsiku limodzi, ndi ndondomeko yomwe imachitika kwa nthawi yaitali. Nanga poti anthu ena kulibeko, ntchito igwirika bwanji? Izi tikudandaula nazo,” adatero Ndanga.

Mogwirizana ndi akulu a zipani ziwirizi, Banda adati kutumizidwa kutchuthi kwa akuluakulu ena komanso kusowa kwa mtsogoleri wa bungweli ndi nkhani yaikulu komanso yodandaulitsa.

“Mwachidule, izi zikutanthauza kuti tilibe bungwe loyendetsa zisankho. Bungweli limakhalapo ngati lili ndi mtsogoleri komanso ena omuthandizira. Ndiye bungwe lilipo?” akudabwa Banda.

Koma mkulu wa nthambi yoona za chuma kubungweli, Linda Kunje, akuti anthu asadandaule chifukwa zonse zilongosoka.

“Palibe chovuta ndipo zipani zisadandaule,” adatero Kunje.

Malamulo a zisankho amati pasadutse miyezi itatu dera lisadachititse chisankho chopeza mtsogoleri chichokereni kapena chimwalirireni mtsogoleri amene adalipo. Kunje aadati akudziwa za izi komabe sangachitire mwina.

“Inde taphwanya lamulo koma sitingachitire mwina chifukwa pali zifukwa zomveka zomwe zatilepheretsa kuchititsa zisankhozi,” adatero Kunje.

Pankhaniyi, Banda adati anthu kumadera amene zisankho zaimitsidwa ali ndi ufulu wosumira bungweli. n

Related Articles

Back to top button