Nkhani

Alandira K14 biliyoni yotukulira maphunziro

Maiko ndi mabungwe omwe amathandiza boma ati apereka thandizo la K14 biliyoni ku unduna wa zamaphunziro zotukulira maphunziro m’sukulu za pulayimale.

Lonjezoli lili mumgwirizano wa pakati paboma la Malawi ndi maiko a Norway ndi Germany kudzanso banki yayikulu padziko lonse ya World Bank ndi bungwe la United Nations Children’s Fund (Unicef).

Haugen: Tiyamba chaka chino

Mbali ziwirizi zidasayinirana mgwirizanowu Lachitatu pasukulu ya pulayimale ya Muzu m’boma la Lilongwe ndipo oyimirira mayiko ndi mabungwewa, Kikkan Haugen, yemwe ndi kazembe wa dziko la Norway adati ndalamazi ziyamba kufika chaka chino.

“Gawo loyamba libwera chaka chino ndipo lichokera ku Norway, World Bank ndi Unicef ndipo gawo lachiwiri lidzabwera 2018 ndipo lidzachokera kudziko la Germany,” adatero Haugen.

Iye adatsindika kuti izi sizikutanthauza kuti maiko ndi mabungwewa ayambiranso kupereka thandizo lomwe ankapereka ku bajeti ya Malawi ndipo adasiya pa zifukwa zosayendetsa bwino ndalama za m’bajeti.

Mkulu wa bungwe la mgwirizano wa mabungwe omwe amayang’anira za maphunziro, Benedicto Kondowe, adati nkhaniyo ndi mayeso aakulu ku unduna wa zamaphunziro ndi boma la Malawi.

“Oyendetsa pulogalamu ya thandizo la mumgwirizanowu akuyenera kuzindikira kuti tsogolo la thandizo lina mtsogolo likhala m’manja mwawo chifukwa ntchito zawo ndizo zingakope mayiko ndi mabungwe ena kuti alowererepo,” adatero iye.

Nduna ya zamaphunziro ndi sayansi Emmanuel Fabiano adati boma la Malawi kudzera muunduna wake lionetsetsa kuti thandizoli labweretsa kusintha mmaphunziro a ku pulayimale m’dziko muno.

“Boma, sukulu ndi makolo atenga nawo mbali pachitukuko chilichonse chomwe chikhazikitsidwe m’mapologalamu a mumgwirizanowu ndiponso liziyesetsa kupereka upangili ndi zofunika kuwonjerapo mmapologalamuwo,” adatero iye. 

Related Articles

Back to top button