Nkhani

Alandira makuponi ‘abodza’ kuchoka ku boma

Mitu ya alimi ena ku Mpemba kwa T/A Somba ku Blantyre yabalalika pomwe auzidwa kuti makuponi omwe alandira ndi achinyengo. Iwo adalandira makuponiwo Lachiwiri pa 27 Novembala ndipo atapita kogula mbewu Lachitatu adauzidwa kuti makuponiwo ndi achinyengo.

Funso lomwe alimiwa amafunsa ndi loti zatheka bwanji kuti kubomako kupezekenso zachinyengo? Pachithunzipo ndi alimi ena omwe tidawapeza. Apa akuti abwerera kogulako ndipo chochita sakuchidziwa. Iwo akuti aletsedwa kugula mbewu ndi fetereza ndipo chiyembekezo chawo chafa.—Bobby Kabango

Related Articles

Back to top button