Nkhani

Alimi avale dzilimbe, kukubwera El Nino

Akatswiri a zanyengo alosera kuti chaka chino pali mantha kuti dziko lino lingakumane ndi nyengo yoipa ya El Nino.

Lipoti la BBC lomwe alitulutsa posachedwapa, zofufuza za ofesi yoona za nyengo ya United Kingdom Met Office zikuonetsa kuti zaka ziwiri zikubwerazi kukhala nyengo yotentha koopsa padziko lonse, zomwe zingapangitse kusintha kwakukulu pa mmene nyengo imakhalira.FARMER

Nalo bungwe loona za mavuto a njala kummwera kwa kwa Africa la Famine Early Warning Systems (Fews-Net) lati mmene zikuonekera nyengo ya El Nino iyamba mosapeneka October mpaka December.

Tikati tione mmene zakhala zikuchitikira mmbuyo, kukakhala El Niño mvula simagwa mmene anthu amayembekezera ndipo ati chaka chino zigawo za kummwera kwa Mozambique, Malawi ndi Zimbabwe mvula itha kuvutiraponso monga zidachitikira mu 2014/15.

Nyengoyi ikudza pamene chaka chino alimi ambiri m’dziko lino akulira chifukwa cha kuchepa kwa mvula, pamene ena mvula idangogwa yochuluka kwa nthawi yochepa ndipo mbewu zawo zidakokoloka.

Kukakhala El Nino mwina mvula imagwa mosadukiza komanso ikadula mwina kumakhala ng’amba kwa nthawi yaitali, zomwe zimakhudza kwambiri alimi.

M’nyengo zovuta ngati zimenezi, ndi alimi okhawo otsata bwino ndondomeko zamalimidwe amene amapezabe phindu paulimi wawo kukakhala El Nino.

Prof. Moses Kwapata wa kusukulu ya zamalimidwe ya Luanar ku Lilongwe akuti zateremu alimi asagone koma ayambiretu kukonzekera ulimi wa chaka chino.

“Ngati sadamalize kusosa akuyenera apange changu ndipo agalauziretu minda yawo. Zikatere pamafunika kuti mvula yoyamba ikamagwa zonse zakumunda zikhale zatha kuti alimi athe kubzala ndi mvula yoyambirira,” adatero Kwapata pouza Uchikumbe.

“Feteleza aguliretu, ndipo adzaonetsetse kuti amuthira panthawi yake. Ngati m’munda mwamera tchire asachedwetse kupalira. Chilichonse chikhale m’chimake. Mlimi wotere ngakhale nyengo yavuta ndiye amene amakolola.”

Kwapata adati ngati mwayi ali nawo alimi akuyeneranso kulima mbewu zosiyanasiyana chifukwa zina zimafuna mvula yambiri pomwe zina sizikonda mvula yochuluka.

Related Articles

Back to top button