Nkhani

Alowerera paesiteti ya Kawalazi

Listen to this article

T/A Kabunduli wa m’boma la Nkhata Bay wadandaula ndi anthu pafupifupi 500 omwe adalowerera ndi kukhazikika paesiteti ya tiyi ya Kawalazi m’bomalo.

Kabunduli wati anthuwa, omwe awutcha mudziwo ‘Joni’(potengera mzinda wa Johannesburg m’dziko la South Africa), ndi aupandu chifukwa sadatsate dongosolo loyenera lopezera malo.

“Anthuwa adandipeza zaka zoposa zisanu zapitazo kupempha malo ndipo ndidawauza dongosolo loyenera, koma zodabwitsa ndi zoti adakalowerera malo a esiteti,” adatero Kabunduli.

Mwambi uja amati tikhale nawo adalanda malo ukupherezera pankhaniyi pomwe Kabunduli akulongosola kuti anthuwa si mbadwa za boma la Nkhata Bay koma ndi obwera kuchokera maboma ena a m’çhigawo cha kumpotochi.

Kabunduli adati ali ndi nkhawa ndi mkanganowu chifukwa esitetiyi ndi mpamba wa anthu ake.

“Ndikuopa kuti mkanganowu ungakhudzenso ntchito za anthu a m’dera langa amene amagwira kuesitetiku,” Kabunduli adatero.

Ndipo DC wa bomali, Fred Movete, adati anthuwa, omwe ambiri mwa iwo amaotcha makala chifukwa derali lili ndi mitengo yachilengedwe, amati adalowerera malowa chifukwa omwe adagula esitetiyi m’zaka za m’ma 1970 sanawapatse makolo awo chipepeso.

Movete adati ngakhale anthu ena akutero, ofesi yake idalandiranso malipoti oti anthuwa si mbadwa za m’boma la Nkhata Bay koma ochokera kumaboma ena.

Iye adalongosola kuti nkhaniyi yakhala ikulowa m’bwalo la milandu kangapo konse makamaka pomwe anthu olowererawa adaphwanya galimoto, kulanda wapolisi mufti (yomwe idapezeka) ndi kuvulaza ogwira ntchito pakampaniyi.

“Padakalipano, tikukambirana ndi mbali ziwirizi kuti tibweretse mgwirizano chifukwa nkhanizi zikafika kukhoti, zinthu zimaonongeka,” adatero Movete.

Poyankhulapo akuluakulu a esitetiyi adati mchitidwewu ndi wobwezeretsa chitukuko mmbuyo.

Wachiwiri kwa mkulu wa kampaniyi, Kenneth Kabaghe, adati anthuwa aika kampaniyi pampani.

Iye adati n’cholinga cha kampani yake kukhala mwabata ndi anthu oizungulira, koma izi zikuvuta ndi anthu a mudzi wa Joni.

Related Articles

Back to top button