Nkhani

Alubino akufuna chilungamo

Listen to this article

Bambo wachialubino ku Ntcheu wati akufuna chilungamo pankhani yake yomwe akuloza chala mkulu wina wabisinesi kuti adamutsekera m’golosale ndi kumubera ndalama zokwana K103 000, komanso kumuopseza kuti amupha.

Kudandaula kwake kukubwera pamene bwalo la Mozambique pa 16 February lidagamula kuti woganiziridwayu alibe mlandu kusiya mkuluyu, yemwe ndi mphunzitsi, ali kakasi, kusowa mtengo wogwira.Albino campaign 1

Apolisi m’dziko la Mozambique ndi Malawi atsimikiza kuti nkhaniyi idazengedwadi m’dziko la Mozambique.

Mkulu wachialubinoyu, Charles Chidambukira Ndau, yemwe akuphunzitsa pa Chilobwe LEA ku Lizulu m’bomali, wauza Tamvani kuti pa 6 February adatsekeredwa m’shopu ya wamalonda wina yemwe adamuopseza kuti amupha akakuwa.

“Ndidapita kukagula malata ndipo ndili m’shopumo, adauza mnzake wogwira naye ntchito kuti atseke zitseko. Kenaka adati ndamuchita chitaka ponena kuti K76 000 yake yasowa.

“Adati nditulutse ndalama zanga zonse ndipo ndidatulutsa K103 000 yomwe ndidali nayo ndipo adandilanda K76 000 ndi kundibwezera K27 000, koma adandilandanso n’kuing’ambang’amba.

“Ndimaganiza kuti anditulutsa, koma sadatero ndipo adayamba kundiopseza kuti andipha. Adandimanga n’kukanditsekera kuchipinda cha shopuyi, yomwe ili mbali ya Mozambique m’malire ndi dziko la Malawi,” adatero Ndau.

Iye adati polingalira kuti tsiku lakufa lafika, adapemphera ndipo mwamwayi zingwe adamumangira zija zidalera. Mwamwayinso adali ndi foni ndipo adaimbira mwana wake kumuuza kuti watsekeredwa m’shopumo ndipo akufuna kumupha.

“Adanditsekera cha m’ma 8 koloko mmawa ndipo anthu amatulukira cha m’ma 11 koloko. Adafuna kuphwanya shopu, kenana apolisi a Mozambique adatulukira kudzandipulumutsa komanso adamumanga yemwe adanditsekerayo ulendo kupolisi yawo,” adatero Ndau, yemwe ali ndi ana 6.

Atachoka kupolisiko, Ndau akuti adapita kupolisi ya Lizulu kumbali ya Malawi kukalembetsa sitetimenti ya momwe nkhaniyi idakhalira.

Amaganiza kuti nkhaniyi ikambidwa m’dziko la Malawi potengera kuti wodandaula ndi woganiziridwa onse ndi nzika za ku Malawi, sizidatero. Bwalo la Villa Ulongwe m’dziko la Mozambique ndilo lidazenga mlanduwo ndipo akuti lidagamula kuti palibe mlandu.

“Pa 15 February ndidalandira uthenga kuti ndipite kukhoti la ku Villa Ulongwe ndipo nditapitako pa 16 February adandiuza kuti chigamulo cha nkhani yanga chidali choti palibe mlandu. Adati nkhani idazengedwa pa 12 February pamene ine sindimadziwapo kalikonse kuti yakambidwa,” adatero mkuluyu.

Ndau adati ngakhale adakagwada kupolisi ya Lizulu, padalibe thandizo ndipo mmalo mwake wapolisi wa ku Mozambique ndiye adachita chotheka kuti ndalama zake amubwezere.

“Yemwe adanditsekerayo atabweza ndalamazo, adadziwitsa apolisi ya Malawi kuti asasainirane ndipo ndalama zonse K103 000 adandibwezera. Pamenepa ndipo pakundidabwitsa ine, ngati palibe mlandu, bwanji adabweza ndalamazo?” akudabwa Ndau.

Mkulu wa polisi ya Lizulu m’dziko la Mozambique, Philip Jackson, watsimikiza kuti nkhaniyi idakazengedwadi ku Villa Ulongwe chifukwa idachitikiranso m’dzikomo.

“Tikagwira anthu amene aba ku Malawi, timawapatsira apolisi anzathu a ku Malawi, nawonso Amalawi akagwira anthu amene apalamula mlandu m’dziko lathu amatipatsira.

“Nkhani mukunenayo idachitikira kuno ku Mozambique chifukwa shopuyo ili m’dziko lathu ngakhale onsewo ndi Amalawi. N’chifukwa tidaitengera kukhoti la ku Villa Ulongwe,” adatero Jackson.

Jackson adati mlandu womwe udapita kubwaloko ndi wotsekera munthu m’nyumba, osati wofuna kumupha, monga mwini wake akunenera.

“Nkhani zofuna kupha anthu achialubino nzovuta ngakhale m’dziko lathu, ndiye tidamutsegulira mlandu wotsekera munthu m’nyumba,” adatero.

Wapolisi wina papolisi ya Lizulu mbali ya ku Malawi, yemwe adati tisamutchule dzina, naye adatsimikiza kuti nkhaniyi idazengedwadi m’dziko la Mozambique koma adati ngati tifuna kudziwa zambiri tiyankhule ndi a kulikulu la polisi.

Wapolisiyu adatsimikizanso kuti Ndau adakadandaula kupolisi yawo koma chomwe adangomva nkuti chigamulo chaperekedwa kale ku Mozambique.

Koma wachiwiri kwa mneneri kulikulu la polisi m’dziko muno, Thomeck Nyaude, wati chomwe akudziwa nkuti nkhaniyi ili m’manja mwa khoti la Malawi.

“Nkhaniyo ndikuidziwa, chomwe ndinganene nkuti nkhaniyi ikalowa m’khoti tsiku lina lililonse. Zoti kwaperekedwa chigamulo ku Mozambique, ine sindikudziwa. Ngati anthuwo ndi Amalawi, zitheka bwanji kuti mlandu wawo ukazengedwe ku Mozambique?” adatero Nyaude, koma sadatchule khoti lomwe lizenge nkhaniyi.

Mkulu wa bungwe la Association of Persons with Albinism, Boniface Massah, wati nkhaniyi akuidziwa ndipo nawonso ndi odabwa ndi chigamulo komanso chifukwa chomwe idakazengedwa m’dziko la Mozambique.

“Tikufuna kumvetsa ngati kuli kovomerezedwa kuti nkhaniyi ikazengedwe m’dziko lina, koma nkhani yathu yaikulu ndi zotsatira za chigamulo kuti adapeza kuti palibe mlandu,” adatero Massah.

Iye adati akudikirabe yankho pa kalata yomwe adalembera unduna woona za anthu olumala yomwe adapempha kuti chigamulochi chiunikidwe asanakamang’ale kubwalo lina.

Related Articles

Back to top button