Nkhani

Amalawi 9.5 miliyoni angakhale akhungu

Listen to this article

Bungwe logwira ntchito zopulumutsa anthu ku vuto la khungu dziko lonse la pansi la Sight Savers lati Amalawi 9.5 miliyoni akhoza kuchita khungu pofika chaka cha 2019 chifukwa cha vuto la matenda a maso otchedwa trachoma.

Chiwerengerochi chikupitirira pang’ono theka la chiwerengero cha anthu onse m’dziko muno chomwe chili pafupifupi 17.2 miliyoni.

Unduna wa zaumoyo watsimikiza za chiwerengerochi koma wati boma lakhazikitsa njira zofuna kuthana ndi vutoli.

Mneneri wa undunawu, Henry Chimbali, adati boma mogwirizana ndi mabungwe omwe si aboma ali kalikiliki kukhazikitsa njira zotetezera anthu omwe ali pachiopsezo choti nkukhudzidwa ndi vutoli.

“Chiwerengerochi tachipeza potengera kukula kwa vutoli padakalipano koma zonse zikayenda bwino ndi njira zomwe takonza chikhoza kutsika,” adatero Chimbali.

Kachilombo kosaoneka ndi maso ka mtundu wa bacteria ndiko kamayambitsa matendawa ndipo zizindikiro zake ndi manthongo, kuyabwa kapena kuwawa kwa maso, kusawona bwino ndi mantha nkuwala.

Oyendetsa ntchito za bungweli m’dziko muno Roy Hauya adati matendawa avuta kwambiri m’maiko 53 ndipo anyanya mmaiko 14 kuphatikizapo Malawi.

Hauya adati amayi ndi ana ndiwo ali pachiopsezo chachikulu pa vutoli chifukwa cha malo omwe amapezeka ndi ntchito zomwe amagwira.

Iye adati padakalipano, anthu 33 000 mwa anthu 9.5 miliyoni omwe ali pachiopsezochi m’Malawi muno akhoza kuchita khungu losachizika ndipo matendawa akula kwambiri m’maboma 17.

Chikalata chomwe bungweli lidatulutsa chasonyeza kuti anthu 10 mwa anthu 100 aliwonse m’maboma 6 momwe vutoli lakukla kwambiri akudwala matenda a masowa ndipo mpofunika changu kuti apulumutsidwe.

Mabomawa ndi Nsanje, Mchinji, Lilongwe, Salima, Kasungu ndi Nkhotakota ndipo chikalatacho chidati anthu 5 902 akufunika opaleshoni yowateteza ku vuto la khungu loyamba chifukwa cha matendawa.

Wothandizira woyendetsa ntchito za chipatala mu unduna wa zaumoyo Michael Masika adati vutoli lingathe anthu atatsatira zomwe bungwe la zaumoyo dziko lonse la World Health organisation (WHO) lidaunikira.

Bungwe la WHO lidaunikira kuti vutoli lingathe kudzera mu maopaleshoni, kugwiritsa ntchito mankhwala ophera tizilombo tomwe timayambitsa matendawa, kusamba mmaso moyenera komanso ukhondo wa pakhomo.

Hauya adati matendawa amafala ndi ntchentche yomwe yatenga tizilombo toyambitsa matendawa kuchoka pa chimbudzi, manthongo kapena mamina a munthu yemwe akudwala matendawa yatera mmaso mwa munthu wina.

Pofuna kuthana ndi vutoli, bungwe la Queen Elizabeth Diamond Jubilee Trust lapereka ndalama zokwana £7.3 miliyoni (pafupifupi K5.2 biliyoni) kubungwe la Sight Savers lothetsera vutoli.

Related Articles

One Comment

  1. I wonder how true this information is, the figures are so alarming and if this is really true then it is almost like an outbreak. 2019 is not so far from now and am surprised if this is not another fundraising gimmick, I mean 9.5 million people being blind, wait a minute….. 9.5 milllion???

Back to top button