Nkhani

Amalawi a nsomba ali kakasi ku Botswana

Listen to this article

Ali mbuu, kutuwa ndi njala, Patricia Mboma ndi wokwiya ndi ganizo la boma la Botswana loletsa kuti m’dzikomo musatuluke nsomba kukagulitsa maiko ena.

Si ali yekha, pali ena a dziko la Zambia komanso Botswana. Onse alipo anthu 60 amene agula nsomba zodzadza mathilaki asanu kupita ku Zambia kukagulitsa.

Zina mwa nsombazo ndi zimenezi

Mboma, wochokera ku Blantyre, adayamba bizinesiyi mu 2014 kukagula nsomba kunyanja ya Ngami moyandikana ndi Maun kumpoto kwa dziko la Botswana.

Koma ulendo uno wakhala wowawitsa kwa abizinesiwa pamene boma laletsa kutulutsa nsomba m’dzikomo ponena kuti silikupindula pa malondawo.

Kuderali anthu ambiri adapeza mgodi wopha ndalama popikula nsomba zouma ndi kukazigulitsa m’dziko la DRC kapena ku Kasumbalesa ku Zambia.

Izi zidachititsa kuti mwezi wa March chaka chino, nduna ya zachilengedwe ndi nyama zakunkhalango Tshekedi Khama, mng’ono wake wa pulezidenti wa dziko la Botswana Ian Khama aletse malondawa.

Pamene amaletsa malondawa, n’kuti Mboma komanso anzake atagula kale nsombazo ndipo sadaloledwe kuti apite kukagulitsa.

Kuyambira March mpaka lero, anthuwa akhala akubindikira ku wadi ya Boseje ku Maun. Sabata yatha adathamangitsidwa pamalopo ndipo akubisala ku Kasani kumalire a Botswana ndi Zambia komwe akukanizidwa kudutsa.

“Tikupempha boma litilole tipite kukagulitsa nsombazi,” adatero Mboma. “Ndaononga P30 000 [K2.2 miliyoni] kuti ndigule nsombazi,” adatero iye.

Nsomba zambiri zayamba kuola, ntchentche zangoumbirira mathirakiwa. “Komabe sindichitira mwina achimwene, ndikuyenera kupita ndi nsombazi ndikagulitse, ndidachita kukongola ndalama yogulira nsombazi. Yochepa yomwe ndingapezeyo ndi yomweyo,” adatero Mboma.

Lero vuto lina labadwa pamene eni galimoto akufuna kuti azipita, malinga ndi mabwana awo. Kelvin Kambule amene akuchokera ku Livingstone m’dziko la Zambia akuti bwana wake wapindira mlomo wapansi.

“Akuimba tsiku lililonse, akuti ndichotse nsombazi ndipo ndizipita. Takhala pano miyezi inayi osapanga chilichonse n’chifukwa chake akwiya,” adatero.

Thilaki iliyonse yanyamula nsomba za P500 000 [K37 miliyoni] ndipo anthuwa akuyenera kulipira P12 000 [K900 000] kuthiraki iliyonse ponyamula nsombazi.

Komabe boma la Botswana laponda mwala kuti silisunthika pa ganizo lake. “Sitilola kuti geniyi ipitirire, mchitidwewu wapangitsa kuti pa nyanja pachuluke asodzi opanda zikalata zowalola kuti aphe nsomba,” adatero Khama.

Izi zipangitsa kuti misozi ya Mboma isaleke kukha: “Tsiku lililonse tikumasonkherana P5 [K370] kuti tidye. Masiku akatha okhalira m’dziko muno tikumapita m’maiko athu kukaonjezeretsa masiku. Adakatimvera chisoni.” 

Related Articles

Back to top button