‘Amalawi atopa ndi boma’

Listen to this article

Kwathina! Zionetsero za pa 27 April zikukolera moto. Nzika zina za Malawi zokhala m’dziko la South Africa, PAC, chipani chotsutsa cha MCP ndi mabungwe omwe si aboma ati adzachita nawo zionetserozo.

Zionetserozi zikuchitika pokhumudwa ndi nkhani ya K4 biliyoni yomwe boma lidakonzekera kugawira aphungu 86 amene adakana bilo yosintha malamulo a chisankho. Otsutsa atapanikiza boma za nkhaniyo, lidasintha thabwa n’kunena kuti ndalamazo azigawa kwa aphungu onse.

Kuchita zionetsero ndi ufulu wa aliyense

Izi zikuchitika pomwe nduna ya zachuma Goodall Gondwe idakana kutula pansi udindo kuti nkhaniyo ayifufuze bwino komanso mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika sadachotse ndunayo kuti zofufuza zichitike.

Mwa mabungwe ena amene alonjeza zotenga nawo mbali ndi a Human Rights Defenders Forum (HRDF), Centre for Human Rights and Rehabilitation (CHRR), Centre for the Development of People (Cedep), Public Affairs Committee (PAC), Youth and Society (YAS) ndi Citizens Forum for the Defense of Good Governance.

Mkulu wa bungwe la Cedep, Gift Trapence adati kupatula nkhani ya K4 biliyoni, nkhani yomwenso yawakwiyitsa ndi kuzimazima kwa magetsi, kukula kwa ulova ndi zina zotero.

“Zionetserozi zichitika m’maboma a Karonga, Mzuzu, Lilongwe, Blantyre, ndi Zomba. Chilichonse chokonzekera zionetserozi chachitika,” adatero Trapence.

Nawo Amalawi 87 okhala m’dziko la South Africa akhala nawo pa zionetsero  pa 27 April.

Mtsogoleri wawo, Mwamikendi Msukwa adati akukonza mabasi amene adzawanyamule kubwera m’dziko muno ndi kudzaonetsa mkwiyo wawo.

“Si nkhani ya K4 biliyoni yokhayo komanso dziko lathu likupita kuphompho. Zinthu zikungokwera mitengo. Tidachoka m’dzikomo osati kufuna koma chifukwa chakuchuluka kwa mavuto,” adatero Msukwa.

Mkulu wa bungwe la CHRR, Timoty Mtambo adati kubwera kwa anthu okhala m’dziko la South Africa ndi chisonyezo choti aliyense akufuna zinthu zisinthe m’dziko muno.

“Nthawi yakwana, Satana achite manyazi. Amalawi atopa ndipo akufuna tsogolo lawo lioneke. Ku Joni kuli mavuto ambiri koma apanga chisankho kuti asabwerenso chifukwa cha mazangazime amene dziko lino likudutsamo,” adatero Mtambo.

Mtambo adati madandaulo awo akawapereka kwa mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika.

“Takhala tikusiya madandaulo athu kudzera m’thambi zosiyanasiyana koma sizidaphule kanthu. Pano tikamupatsa pamanja,” adatero.

Nduna ya zofalitsa nkhani Nicholas Dausi adakana kuthirirapo ndemanga koma mneneri wa Mutharika, Mgeme Kalilani wati izi sizingatheke kuti Mutharika akalandire kalatayo kuchokera kwa iwo. Izi zakhumudwitsa Mtambo.

“Apa zikuonekeratu kuti mtsogoleriyu siokonzeka kutumikira anthu ake. Amathawa kukayankha mafunso m’Nyumba ya Malamulo, pano akutithawanso. Ili ndi tanthauzo kuti sakukwanira pa utsogoleri,” adatero Mtambo.

Zionetserozi zomwe zikuchitika pa mutu woti ‘Mpaka liti Amalawi adzatengedwe kumtoso’ zalandiranso moto kuchokera ku bungwe la amipingo loona za momwe zinthu zikuyendera la PAC.

Mkulu wa bungwelo mbusa Felix Chingota wati mfundo zomwe akunena a mabungwewa ndi zomveka ndipo Amalawi ayenera kuonetsa ufulu wawo.

Mtsogoleri wa chipani chotsutsa cha Malawi Congress (MCP), Lazarus Chakwera adavomereza kale kuti achita nawo zionetserozo monga momwe adalankhulira m’Nyumba ya Malamulo.

Zinthu zidalakwikanso Lamulungu lathali pamene Synod ya Nkhoma idatulutsa chibaluwa chodzudzula utsogoleri wa dziko lino chomwe chidawerengedwa m’matchalitchi ake.

Mwa zina, chibaluwacho chidadzudzula utsogoleri wa chipani cha DPP kuti sukuganizira anthu osauka ndipo chachenjeza anthu kuti adzavotere molondola m’chisankho cha 2019.

Chibaluwacho chidakambanso za magulidwe a majenereta, kusakaza chuma chaboma, ziphuphu ndi zina.

Related Articles

Back to top button