Chichewa

Amanga wometa mnzake kumanyazi

Zachilendo akuti zachitika ku Mangochi komwe apolisi amanga mkulu wina pomuganizira kuti adameta mnyamata wa fomu 4 malo aulemu.

Mneneri wa polisi ya Mangochi Rodrick Maida watsimikiza za kumangidwa kwa Kenneth Chimombo, wa m’mudzi mwa Mtalimanja, kwa T/A Mponda m’bomalo.

Maida wati apolisi amutulutsa mkuluyu pabelo pamene kufufuza zenizeni za nkhaniyi kukupitira. Iye akuti amutsekulira mlandu wogwira munthu malo osayenerera (indecent assault).

arrest

Maida adati Chimombo adakumana ndi mnyamatayo Lachitatu pa 23 March pomwe adagwirizana kuti akachezerane.

“Mnyamatayo adauza apolisi kuti wakhala nthawi asakupita kunyumba kwa Chimombo ndipo patsikulo atakumana, Chimombo adamuuza kuti abwere kunyumba kwake kuti akacheze,” adatero Maida.

Cha m’ma 10 koloko mmawa wa tsikulo, mnyamatayo, amene ali ndi zaka 18, akuti adapita kunyumbako ndipo adamupeza Chimombo ndi mwana wina kunyumbako.

Maida adati mnyamatayu wauza apolisi kuti adauzidwa ndi Chimombo kuti apite kuchipinda komwe ati kudachitika zoda mutuzi.

“Akuti panthawi yomwe amauzidwa izi, thupi lake lidafooka, zomwe zidamuchititsa kuti achite chilichonse chomwe amalamulidwa.

“Kuchipindako akuti adayamba kumusisita pamimba ndipo adayamba kumumeta pamimba. Akuti panthawiyi adafooka ngati wabaidwa jakisoni wa dzanzi. Akumumeta choncho akuti adadzidzimuka pamene Chimombo adayamba kumugwira malo obisika kuti amumete,” adatero Maida.

“Apa akuti ndi pamene adazindikira ndipo adatuluka m’nyumbamo ulendo kukanena kwa makolo ake. Panthawiyo akuti adayamba kusanza ndipo adafooka kwambiri.”

Makolo a mnyamatayu akuti ndiwo adapita ndi mwana wawo kupolisi ya Mangochi kukadandaula kuti awametera mwana wawo.

“Kupolisi adavula kuti tione, ndipo tidaonadi kuti adali wometedwa. Ndiye tidamanga Chimombo tsiku lomwelo pomuganizira kuti wachita izi ndi iye chifukwa ndiyenso amatchulidwa,” adatero.

Koma Chimombo, wa zaka 29, akuti wauza apolisi kuti adametadi ndi iyeyo pamene adauzidwa ndi mnyamatayu kuti amumete.

“Sadakane kupolisi, iye wati adachita kutumidwa ndi mnyamatayu kuti amumete. Tidamutengeranso kubwalo la milandu komwe amakauzidwa za mlandu womwe akuzengedwa,” adaonjeza Maida.

Ngati Chimombo akapezeke wolakwa pamlanduwu, atha kukakhala kundende zaka zitatu, malinga ndi malamulo a dziko lino.

 

Related Articles

Back to top button