Amangidwa popha ‘anamapopa’

Ndende ya Nsanje ikusunga anthu awiri omwe akuyenera kuyankha mlandu wopha Landani Chipira wa zaka 48 atamuganizira kuti ndi ‘namapopa’ m’mudzi mwa Gulupu Mchacha James kwa T/A Mlolo m’bomalo.

Malingana ndi mneneri wapolisi ya Nsanje Agnes Zalakoma, anthuwa, omwe sadawatchule maina poopa kusokoneza kafukufuku wawo, adaonekera mukhoti Lachiwiri ndipo mlandu udzapitirira pa 20 October 2017. Koma kafukufuku wa Tamvani wapeza kuti awiriwo ndi gulupu ndi mfumu ina kumeneko.

An artist’s impression of the arrest

Zalakoma adati anthu a m’mudziwo adakwiya ndi machitidwe a Chipira, yemwe anali mfumu Chizinga, ngati ‘namapopa’ ndipo adamugenda mpaka kupha.

“Masana apa 28 September, anthu olusa adathyola nyumba ya mkuluyo ndi kumugenda. Kufika lero, tamanga anthu awiri powaganizira kuti akukhudzidwa ndi imfayo. Sitiwatchula maina awo kuopa okhudzidwa ena angathawe,” iye adatero.

Pa nkhani yomweyi, mneneriyu adati apolisi amanganso amayi awiri a m’mudziwo, Chrissy Goba ndi Nota Tomas powaganizira kuti adafalitsa mauthenga abodza odzetsa mantha mwa anthu zomwe ndi zosemphana ndi gawo 60 la malamulo a zilango m’dziko muno.

Mbusa Danger Giant, wa mpingo wa Open Door m’dera La Gulupu Mchacha James, adati chibwana chalanda ndipo anthu akudandaula chifukwa chotaya moyo wa mfumu pa mpheketsera chabe.

“Munthu wina m’mudzi mwa malemuwa adati wapopedwa magazi ndiye ambiri adangoti mfumu ikudziwapo kanthu ndi kukayigenda. Chibwana ndi kuchita zinthu m’chigulu zadzetsa chisoni m’mudzimo,” adatero Giant.

Kumangidwa kwa awiriwo kudadza pomwe mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika adadzudzula mchitidwe wopha anthu oganiziridwa kukhala a namapopa. Pamsonkhano wandale, Mutharika adakonza zokayendera maboma amene mchitidwewu wakula m’chigawo chakummwera monga Mulanje, Phalombe, Thyolo ndi Nsanje.

Mutharika adati: “Ndakhudzidwa ndi zopopana magazi. Amalawi mitima ikhale pansi. Tiyenera kupewa kufalitsa nkhanizi chifukwa zilibe umboni ndipo n’zopweteketsa anthu osalakwa.”

Anthu 7 aphedwa kale poganiziridwa kuti ndi anapopa zimene zachititsa dziko la United States of America komanso bungwe la United Nations kuchotsa ogwira ntchito ake m’madera okhudzidwa.”  

Zoonjezera: BOBBY KABANGO

Share This Post