Nkhani

Ambwandira msilikali ku Salima

Apolisi a chigawo chapakati abatha msilikali wa nkhondo ndi anthu ena awiri powaganizira kuti adapezeka ndi chamba popanda chilolezo.

Msilikaliyu, Alex Kanjanga wa zaka 23 wagwidwa ndi majumbo 16 a chamba pachipikisheni cha polisi pa Thavite m’boma la Salima.

Mneneri wa polisi m’chigawo chapakati Noriet Chihana—Chimala watsimikiza za nkhaniyi ndipo wati tsiku lomwe msilikaliyu adagwidwa pa 3 April 2018, apolisiwo adagwiranso Lawrent Medson Tambala wa zaka 30 atamupeza ndi majumbo 11 achamba komanso Mary Mwambane wa zaka 28 atamupeza ndi katundu yemwe akuganiziridwa kuti adabedwa.

Chimala wati apolisi adakhazikitsa malo achipikisheni adzidzidzi pa Thavite ndipo katundu yenseyo adapezeka pachipikishenicho ndipo anthu onsewa akawonekera ku khoti kafukufuku akatha.

Kanjanga yemwe akugwira ntchito ku Engineers Battalion yomwe ili m’boma la Kasungu amachokera m’mudzi mwa Msongola kwa mfumu Kwataine m’boma la Ntcheu.

“Tidamupezanso ndi njere za chamba,” adatero Chimala.

Iye adati pamalopo, adagwiranso Tambala akuchokera ku Nkhotakota ndipo iye adabisa majumbo achambawo m’chikwama chomwe amayenda nacho paulendowo.

Malingana ndi Chimala, Tambala amachokera m’mudzi mwa Kapangalika, kwa mfumu Khongoni m’boma la Lilongwe ndipo naye akuyembekezera kafukufuku wapolisi kuti akawonekere ku khoti.

Awiriwa awatsegulira mlandu wopezeka ndi chamba popanda chilolezo chilichonse.

Pachipikisheni china patsikulo, apolisi adapeza zipangizo zowotchererera m’chikwama cha Mwambane koma iye adalephera kufotokoza komwe adatenga zipangizozo ndipo apolisiwo adamutengera ku polisi ya Salima.

“Ndi ntchito yapolisi kulondoloza komwe katundu wachokera, ngati munthu akulephera kuonetsa malisiti ogulira kapena kufotokoza bwino komwe watenga katundu yemwe alinaye, amayenera kutengedwa kuti akalongosole bwino za katunduyo,” watero Chimala.

Mwambane amachokera m’mudzi mwa Mbuna, kwa mfumu Kanyenda m’boma la Nkhotakota ndipo akuyembekezeka kudzayankha mlandu wopezeka ndi katundu oganiziridwa kuti adabedwa kafukufuku wapolisi akatha.

Related Articles

Back to top button