Chichewa

Anachezera

Listen to this article

Zidatheka!
Zikomo Anatchereza,
Ndafuna ndikuthokozeni kwambiri chifukwa cha malangizo anu. Pano tidamanga banja ndi mtsikana wa ku Machinga uja ndipo pano tikukhala ku Phalombe bwinobwino. Ndathokoza pondithandiza maganizo.
Chifundo Makisi,
Phalombe

Zikomo a Makisi,
Nkhani yosangalatsa! Inenso ndathokoza kwambiri kuti mutatsatira malangizo anga mwalongosola zonse za banja ndipo pano zonse zatheka bwinobwino. Zonyandiritsa kwambiri. Izi ndi zimene timafuna, paja amati mutu umodzi susenza denga. Munthu ukazingwa umayenera kupempha nzeru kwa ena monga akuluakulu ndipo nthawi zambiri malangizo awo amakhala aphindu ukawatsatira. Ndiye ndasangalala zedi kuti ndinatha kukuthandizani pamoyo wanu wa banja. Ambuye akutsogolereni m’zonse kuti banja lanu likhale lolimba ndiponso langwiro komanso lachitsanzo kwa ena.

Amanditukwana
Ine ndidapeza mwamuna woti timange banja koma tikuyendetsa chibwenzi, khalidwe lake amangonditukwana ndi abale anga ngati anafuna kuti tionane ine n’kulephera. Agogo, ndithandizeni, kodi pamenepa nditani?
AM
Area 49, Lilongwe

Zikomo AM,
Pa Chichewa pali mawu oti ‘ali dere n’kulinga utayenda naye’. Ndikhulupirira tanthauzo la la mawu amenewa umalidziwa. Mwachidule, ndinene kuti kufunikira kokhala pachibwenzi anthu musanakwatirane n’koti mumatha kudziwana makhalidwe ndi zofuna musanaganize zolowa m’banja. Khalidwe ndi lofunika kwambiri paumunthu. Tsono munthu wakhalidwe labwino ungamudziwe bwanji? Munthu wakhalidwe labwino ndi woti sachita kapena kunena zinthu zodandaulitsa kwa ena. Wakuba, wachiwerewere, wotukwana, wamiseche, waumbombo kapena wochita zinthu zina zolaula tinganene kuti ndi wamakhalidwe abwino? Osatheka! Ndiye apa wadzionera wekha khalidwe la bwenzi lakolo—kukonda kutukwana. Kodi mukadzakwatirana adzasintha khalidwe limenelo? Kaya! Uyu wadzionetsa kale mawanga ake ndipo usataye naye nthawi, musiye chifukwa si munthu womanga naye banja ameneyo. Munthu wotukwana mkazi kapena abale ake ndi munthu wopanda khalidwe. Ndiye iyeyo ungalimbe mtima kukwatirana ndi munthu woteroyo? Ine ndikuti asakutayitse nthawi, peza wina wamakhalidwe abwino.

Ndinalakwitsa kumuuza?
Agogo,
Ndakhala pachibwenzi ndi mkazi wina kuyambira 2012 koma pamene ndinkamufunsira nkuti ndikumwa ma ARV koma chaka chino mpamene ndamuuza kuti ndili choncho. Padalibe kusintha pachikondi chathu koma vuto lidabwera atapita ku Blantyre. Ali konko andandiuza kuti adakayezetsa magazi ndipo sadamupeze ndi kachilombo ka HIV. Kuchokera pompo chikondi chidasintha, sitimakondana monga mwakale moti pano adakali ku Blantyre. Kodi mwina ndidalakwitsa kumuuza za mmene ndilili? Chonde ndithandizeni.
Ine mwana wany MK
Mzuzu

MK,
Chimene udachitacho pomuuza bwenzi lako mmene ulili ndi chinthu cholondola ndithu ndipo udachita bwino kwambiri ngakhale kuti udatenga nthawi yaitali usamuuze chilungamo. Mwina zikadakhala bwino koposa udakamuuza poyambirira pomwe mu 2012. Kuuza mnzako wachikondi za mmene ulili m’thupi mwako cholinga chake chimakhala choti apange chisankho pamoyo wake—ngati ali wokonzeka kupitiriza chibwenzi kapena kulowa m’banja ndi munthu wotere kapena ayi. Ali ndi ufulu wotere. Choncho, ngakhale ndi nkhani yokhumudwitsa kuti chikondi chanu chazilala panopa chifukwa choti udamuuza zoona za mmene ulili m’thupi mwako, usadandaule. Chikondi sachita kukakamiza, komanso pamene pali chikondi chenicheni palibe mantha. Ndiye ngati bwenzi lakolo lasintha maganizo malingana ndi nkhani yoti uli dere, musiye, zikhale choncho, si mathero a dziko. Ingozivomera chifukwa Mulungu ali ndi cholinga pa chilichonse chimene chimatichitikira pamoyo wathu. n

Related Articles

Back to top button
Translate »