Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

 

Kwawo sindidziwako

Agogo,

Ndinapeza mwamuna kudzera patsamba lino ndipo ndikuyamika chifukwa chondithandiza. Komano vuto langa ndi loti amakana kuti ndikadziwe kwawo, koma kwathu anapitako. Kumuuza kuti abwere ndi akwawo amati amakhala kutali. Ine ndimakhala ku Blantyre ndipo mwamunayo amakhala ku Lilongwe. Kodi ndiziti ndili pabanja?

Ndine NF,

Balaka

Zikomo NF,

Ndasangalala kuti munatha kupeza mwamuna kudzera patsamba lino. Zimatere bwenzi zikoma! Chomwe ndingakulangizeni n’chakuti pamakhala dongosolo polowa m’banja. Kupeza mwamuna kapena mkazi ndi sitepe yoyamba imeneyo ndipo musanalowe m’banja pamafunika zinthu zingapo zichitike malingana ndi miyambo ndi chikhalidwe cha mtundu wanu.

Pakati pa Achewa ndi mitundu ina yambiri chigawo chapakati ndi ndi kummwera, ankhoswe a mbali zonse ziwiri—akuchimuna ndi akuchikazi amayamba akumana kaye kuti adziwane kenaka amakonza chinkhoswe. Chinkhoswe chikatheka kwatsala ndi ukwati kapena mukhozanso kulowa m’banja malingana ndi mmene mwazikonzera.

Tsono ngati mwamuna wanuyu akukana kapena sakufuna kuti mukadziwe kwawo komanso akukana kubwera ndi akwawo, chilipo chimene akubisa. Munthu wotere nthawi zambiri amakhala kamberembere ndipo musamudalire kuti ali ndi chidwi ndi banja ameneyo. Munthu wachilungamo sasowa maonekedwe ndi machitidwe ake, koma uyu yekha ndikuona kuti ndi kapsala basi, musamale naye. N’kutheka kuti mwina ali kale ndi mkazi ameneyo ndipo akuopa kuti mukapita kwawo mukatulukira chinsinsi chake.

Mawu anga otsiriza ndikuti pokhapokhapo atalola kuti mukadziwe kwawo kapena abwere ndi akwawo kudzatomera ukwati, ndi bwino kusiyana naye ameneyo chifukwa adzangokutayitsani nthawi pachabe.

Samayankha foni

Anatchereza,

Ndili ndi chibwenzi ndipo tidagwirizana zomanga banja mtsogolomu. Iyeyu ndidakumana naye kumudzi kwathu komwe kuli makolo ake koma kwawo ndi ku Chitipa. Tsiku lina bwenzi langalo adanditsanzika kuti akupita kumudzi kwawo kuukwati wa mbale wake ndipo adandipempha kuti ndimugulire foni kuti tizilumikizana mosavuta poti yomwe adali nayo idali yovuta. Ine sindinavute, ndinamugulira foni yanyuwani. Kenako adandipempha ndalama yodyera komanso yoti agulire simukhadi ndipo nditamufunsa kuti akufuniranji simukhadi ina pomwe ina ilipo, adandiyankha kuti nambala yakale sakuifunanso. Sindinawiringule koma kumuchitira zomwe amafunazo chifukwa ndimamukonda. Koma chodabwitsa ndi choti atagula simukhadiyo sadandiuze nambala yatsopanoyo mpakana adanyamuka ulendo wakwawo. Padapita sabata ziwiri ndisakuidziwa nambala yanyuwaniyo ndipo kuti ndiziidziwa ndidachita kukafunsa kwa mayi ake. Kumuimbira sakuyankha ndipo ndikunena pano patha chaka tisakuyankhulana. Koma chodabwitsa nambala yanga adakagawa kwa azibale ake ku Chitipako ndiye ndiziti chiyani pamenepa, chikondi chidakalipo? Chonde ndithandizeni.

YK,

Lilongwe

 

Okondeka a YK,

Inde, mukhozadi kudabwa ngatidi pali chikondi pamenepa. Inenso ndikukaika ngati bwenzi lanulo ndi lachindunji. Nanga chosinthira nambala ya foni koma osakuuzani inu bwenzi lake ndi chiyani? Nanga mpakana cha psiti osayankhulitsana anthu oti muli pachibwenzi pali chilungamo pamenepo? Kusonyeza kuti anthu mumakondana mumayankhulana nthawi ndi nthawi n’kumakamba tinkhani tanu tachikondi n’kumalimbikitsana kuti ngakhale mwatalikirana palibe chomwe chingakupingeni pachikondi chanu. Eetu, anthu mukatalikirana mpamene mumalakalakana ndi kusowana. Ndi mmene zimakhalira. Tsono n’tafunsa, kodi abale ake kapena makolo ake akuti chiyani mukawafunsa za bwenzi lanulo kuti sakukuyankhani mukamuimbira foni? Mwinatu akudziwapo kanthu. Koma mosakutayitsani nthawi, iwalaniko za iye ndipo yang’anani wina wachikondi, uyo sali ndi chidwi ndi inu.n

Related Articles

Back to top button
Translate »