Chichewa

Anatchezera

Listen to this article

Ndimamukonda

Agogo,

Ndinali pachibwenzi ndi mkazi wina ndipo zaka ziwiri zatha pomwe tinasiyana. Pano ali ndi mwana yemwe wabereka mwezi watha ndiye akumabwera kwa ine n’kumati tibwererane. Kodi pamenepa ndithani, agogo? Mkaziyo kunena zoona ndimamukonda, koma pano ndinalimba mtima. Nditani?

Ine Amfumu,

Zingwangwa

Amfumu,

Nkhani yanu ndi yovuta kuitsata bwinobwino chifukwa simukumasula kuti vuto lanu ndi chiyani kwenikweni. Poyamba mwanena kuti mkaziyo munasiyana naye zaka ziwiri zapitazo, munasiyana chifukwa chiyani? Mwati pano mkaziyo akuti mubwererane ndipo inu nomwe mukuti ‘kunena zoona ndimamukonda’. Komanso inu nomwenso mukuti pano munalimba mtima, mukutanthauzanji? Mwatinso mkaziyo ali ndi mwana wa mwezi umodzi, n’chachidziwikire kuti mwanayo si wanu-poti mwanena nokha kuti chibwenzi chanu chidatha zaka ziwiri zapitazo. Apatu, kunena zoona, Amfumu, mayankho muli nawo ndinu. Ngati mkaziyo mukuti mumamukonda, chovuta n’chiyani kuti mubwererane? Koma mukuti mwalimba mtima, kulimba mtima kotani? N’chifukwa chake ndikuti zonse zili ndi inu kuti mubwererane kapena ayi poti zifukwa zake zomwe mudalekanirana mukuzidziwa ndinu. Mwakula mwatha, Amfumu.

 

Akungosereulana nane?

Anatchereza,

Ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina amene ndikufuna kukwatira koma zochitika zake zikundidabwitsa. Chaka chatha adandijejemetsa pamene adati ali ndi mimba ndipo amati akufuna achotse chifukwa akuopa makolo ake. Ndidamuuza kuti asayerekeze kuchotsa pathupipo chifukwa ine ndidali wokonzeka kumukwatira, zivute zitani. Kenaka, patapita kanthawi adati amangocheza, alibe mimba. Mwezi wathawu adandiza kuti adakayezetsa magazi ndipo amupeza ndi kachilombo ka HIV ndipo n’kofunika kuti nane ndikayezetse. Kunena zoona, sindinapite kukayezetsa koma ndidangomunamiza kuti ndakayezetsa ndipo sanandipeze ndi kachilombo. Pano wandiuza kuti amangonama, sadakayezetse magazi. Kodi iyeyu ndi mtsikana wotani? Ndipitirize naye chibwenzi?

YB,

Lilongwe

 

Zikomo YB,

Pali zinthu ziwiri: Bwenzi lakolo mwina ndi wokonda kusereula komanso mwina ndi kamberembere. Koma zili ndi iwe kupeza choona chenicheni mwa iye. Koma tiyeni tione mbali zones ziwirizi. Poyamba, ngatidi amakonda kusereula, umuuze kuti pali zina zoti angathe kusereula nawe koma nkhani za mimba ndi HIV si nkhani zosereula nazo. Ngati akufuna aone ngati umamukondadi pali njira zina, osati kunamizira mimba kapena kuti amupeza ndi kachilombo. Kusereulana si kolakwika mukakhala pachibwenzi chifukwa ndi njira ina yokometsa chibwenzi chanucho, koma pali malire. Komanso mwina, monga ndanena, akhoza kukhalanso kamberembere ameneyo. N’kutheka mwina adachotsadi mimba ameneyo. Ngati adaterodi, cholinga chake chidali chotani? Wofuna banja amachotsanso pathupi mwadala? Ayi. Tsono pankhani yokayezetsa magazi, bwanji mutapita kuti mukayezetse limodzi kuti mudziwe momwe mulili nonse? Kwa anthu ofuna banja lansangala, losakaikirana, kuyezetsa magazi ndi njira imodzi yothandiza kuti mudziwe ngati muli ndi kachilombo pena ayi. Mukatere mumadziwa chochita pankhani ya kasamalidwe ka banja lanu.

Related Articles

Back to top button
Translate »