Chichewa

ANATCHEZERA

Sitinakumanepo

Anatchereza,

Ine dangwa m’chikondi ndi munthu woti sindinakumanepo naye. Ndili ndi zaka 23 koma iye ndikamufunsa zaka zake samandiuza. Ati anandiona pa Facebook. Iyeyu kwawo akuti ndi ku Karonga ndipo akuti akundifuna banja. Nditani pamenepa, gogo wanga? Foni amandiimbira tsiku ndi tsiku ndipo nkhani yake imakhala yoti “ubwera liti kuno, ndakusowa”.

E MP

Blantyre

 

E MP,

Samala, mwana wanga, ndi chikondi cha pa Facebook. Ambiri anong’oneza nazo bondo zoterozo. Palibe vuto kuti wachikondi wakoyo mudakumana pa Facebook, koma vuto limene ndikuona ine ndi loti wayamba kukamba za banja pomwe simudakumanepo. Banja si chinthu choti lero ndi lero chatheka, ayi. Musanamange banja choyamba mudziwane bwinobwino makhalidwe, kenaka makolo kapena achibale mbali zonsezonse nawonso adziwane ndipo mukatsimikiza za chikondi chanu mpamene mumayamba kukamba zomanga ukwati. Osati kungoonana pa Facebook basi muli tikwatirane! Tsono iyeyu umuuze kuti ngati akukufunadi ukwati abwre kwanu, osati iwe upite kwawo. Munthu wachikondi choona amaoneka machitidwe ake, uyo angofuna akuvule, kenako adzati basi sakukufunanso. Amuna otere samalani nawo.

 

Adachotsa mimba

Anatchereza,

Ndimakhala ku Lilongwe ndipo ndinakwatira chaka chatha koma mkazi yemwe ndinakwatirayo nthawi yambiri wakhala ali ku Blantyre kenaka ndinamuitanitsa kuti tidzamange banja. Atabwera ku Lilongwe banja linayambika. Kunena zoona anandioetsa chikondi koma amandikaniza kuti ndikagwire ntchito ku Blantyre akuntchito akandituma moti ndalepherako katatu konse. Koma kachinayi sindinamuuze kuti ndikupita ku Blantyre. Nditafika kumeneko ndi kufufuza za iye ndinamva kuti adakwatiwa koma adachita chothawa kupita ku Lilongwe komwe adapeza mwamuna wina koma atachotsa mimba. Nditani pamenepa?

MN

Lilongwe

 

Zikomo MN,

Monga ndakhala ndikulangiza amuna ambiri opupuluma polowa m’banja, inunso vuto lanu ndi lomwelo—lothamangira kukwatira mkazi woti simunamudziwe kwenikweni. Amati kuona maso a nkhono n’kudekha, koma amuna ambiri amaona kuchedwa ndipo amalowa m’banja mwachimbulimbuli ndipo mapeto ake ndi monga zimene mwamvazo. Maukwati ambiri masiku ano salimba chifukwa cha nkhani ngati zimenezi. Paja masiku ano kuli mafoni a m’manja, Facebook, WhatsApp, Twitter ndi zina zotere pa Intaneti ndipo achinyamata ndi akulu omwe akupeza zibwenzi pogwiritsa njira zamakonozi kupeza zibwenzi. Njirazi si zoipa konse, koma chimene chimafunika ndi kufatsa; mudziwane bwinobwino kaye; kenaka zonse zimakhala myaa! Koma apa poti zachitika kale, ndipo mukuti mkazi wanuyo akuonetsa chikondi, mukondenibe. Banja ndi limenelo, poti chikondi ndicho chimamanga banja. Komanso, dziwani izi: Mamveramvera amapasula banja.

 

Ofuna mabanja

 

Ndine mwamuna wa zaka 27 ndipo ndikufuna mkazi wokongola woti ndimkwatire. Mkaziyo akhale wa zaka pakati pa 21 ndi 24, woti adalemba kale mayeso ake a MSCE komanso wopanda mwana. Ngati ali pantchito zitha kukhalanso bwino kwambiri. Omwe angandifune andiyimbire pa 0884 322 798.

 

Ndili ndi zaka 36 ndipo ndikufuna mkazi wofuna banja wa zaka za pakati pa 25-34 wamwana mmodzi pena awiri koma woopa Chauta. Wotsimikiza aimbe 0888 744 701/

0993 101 112.

 

Ine ndili ndi zaka 24 ndipo ndikufuna mkazi wa zaka zosaposera 23 wochokera chigawo chapakati. Akhale ndi mwana mmodzi kapena ayi chifukwa ine ndili ndi mwana wa zaka zitatu. Nambala yanga ndi 0998 599 766.

 

Ndine mayi wa ana awiri ndipo ndili ndi zaka 32. Ndinapezeka ndi kachilombo ka HIV, koma ndikufuna mwamuna wa zaka za pakati pa 33 ndi 39 woti ndimange naye banja. Akhale wasiriyasi. 0885 342 582/0991 111 279.

 

Ndine mwamuna wa zaka 37 ndipo ndikufuna mkazi wa zaka 25-35. Ndili ndi HIV koma ndimamwa mankhwala. Wosangalatsidwa ayimbe pa 0885 353 117.

 

 

Related Articles

Back to top button
WordPress › Error

There has been a critical error on this website.

Learn more about troubleshooting WordPress.