Chichewa

Anatchezera

Sakufuna kukayezetsa

Anatchereza,

Ndakhala ndili pachibwenzi ndi mtsikana wina kwa chaka chimodzi ndipo timakondana kwambiri. Ndine Mkhristu ndipo ndikhulupirira kuti sibwino kumagonana ndi wachikondi wako musadalowe m’banja lomanga. Ndakhala ndikumva malangizo oti masiku ano ndi bwino kukayezetsa magazi musanaganize zolowana, koma mnzangayu nditamuuza zimenezi adati “ine zimenezo ndiye ayi”. Kumufunsa chifukwa chake adati ineyo ngati ndikudzikaikira ndipite ndikayezetse, osati iyeyo. Akuopa chiyani?

MCJ

Lilongwe

 

Zikomo MCJ,

Mwafunsa bwino! Akuopa chiyani ameneyo? Pali bii, pali munga, ife akale timatero. Chilipo chimene akuopa chifukwa akanakhala kuti ali bwinobwino, si bwenzi akuchita kukanira patalitali kuti ‘ine toto, pita wekha’. Kudziwa mmene munthu ulili usanalowe m’banja ndi chinthu chabwino kwambiri, makamaka masiku ano pamene kuli mliri wa kachilombo ka HIV/Aids. Mundimvetse bwinobwino pamenpa: si kuti munthu akapezeka ndi HIV ndiye kuti sayenera kukwatira kapena kukwatiwa, ayi. Munthu aliyense ali ndi ufulu wokhala pabanja, koma zimakhala bwino kudziwa mmene m’thupi mwako mulili pofuna kukonza tsogolo la banja lanu. Ngati wina apezeka ndi kachilombo kapna matenda ena alionse mumadziwa chochita pofuna kudziteteza kuti nonse mukhale moyo wathanzi. Komanso ngati mukufuna mwana m’banja mwanu madotolo amadziwa njira zokuthandizirani kuti mwana wanu asatenge nawo kachilomboko. Chachikulu ndi chikondi pakati panu-pali chikondi palobe mantha. Mufotokozereni wokondedwa wanuyo zimenezi kuti amvetsetse, koma ngati akumenyetsa nkhwangwa pamwala, musiyeni ameneyo, muyang’ane wina amene angakumvetsetseni pankhani yoyezetsa magazi.

 

Nsalu ya lekaleka Anatchereza,

Ine ndi mwamuna wanga takhala pabanja zaka ziwiri ndipo nthawi yonseyi takhala tikugwiritsa ntchito njira zolera chifukwa mwamuna wanga amati nthawi yoti tikhale ndi mwana sinakwane-titoleretolere kaye kuti tisadzavutike tikadzakhala ndi mphatso ya mwana m’nyumba mwathu. Kunena zoona zimene amati titoleretolere kaye sindikuziona, komanso anthu kunjaku ndiye akumatiseka ndi kumatinyogodola kuti sitibereka, ati mwina amunanga adakakhomera ku Dowa. Ine ndiye ndatopa nazo zimenezi.

KB

Mzimba

 

Zikomo KB,

Nkhani yanu ndi yovuta kuimvetsa, komabe ndikuthandizani. Choyamba, kodi pamene mumagwirizana zomanga ukwati wanu, mudayamba mwakhala pansi n’kukambirana za mapulani anu pa nkhani yokhala ndi ana kapna izi munagwirizana mutalowana kale? Ndikufunsa chifukwa ukwati ndi anthu awiri. Ine ndikuona ngati mwamuna wanu chilipo chimene sakufuna kuti mudziwe ndipo akunamizira kuti nonse mukulera. Zaka ziwiri mukutolera za mwana? Mukutolera chiyani? Mwanena kale kuti palibe chimene mukuona kuti mwatolerapo mpakana pano. Mumufunse ameneyo kuti nthawi yakwana tsopano kuti mulandire mphatso yomwe mwakhala mukuiyembekeza ija. Mumuuze kuti simupanganso zolera koma zenizeni, mumve chimene ayankhe. n

Related Articles

Back to top button