‘ankawerenga nkhani pa mij’

Ndi mawu okha, MarcFarlane Mbewe wa Capital Radio adachiritsidwa. Awa ndi makumanidwe a mnyamatayu ndi Lisa Lamya, mtolankhani wa Yoneco FM (YFM).

Nkhaniyi idayamba mu 2014, apo n’kuti Lisa akugwira ntchito ku MIJ FM. Kumeneko, namwaliyu ankawerenga nkhani.

Lero ali ndi mwana mmodzi, Evan: Macfarlen ndi Lisa

Ena mwina amangomva namwaliyo akamawerenga nkhani, koma kwa MarcFarlane, zimamupatsa uthenga wina.

“Mawu ake ozuna komanso Chingerezi chake chothyakuka zidanditenga mtima,” adatero MarcFarlane. “Ndidafunitsitsa nditapalana naye ubwenzi. Mwachangu ndidamusaka pa Facebook. Ndidamutumizira pempho kuti akhale mnzanga.”

Macheza akuti adayamba. Koma mnyamatayo atapempha nambala, Lisa adamukaniza.

“Ndidaponya mfundo ndipo mapeto ake adandipatsa nambalayo,” adatero.

Apo zidayamba kusongola ndipo mathero ake kudali kukumana pamene mfundo zenizeni zidaumbidwa.

Lero Lisa akubwekera posankha mnyamatayu. “MarcFarlane ndidamukonda chifukwa ndi ndi wanthabwala zedi koposa zonse amakonda kupemphera,” idatero njoleyo.

Pamene MarcFarlane akuti: “Lisa ndi mkazi wokoma m’maso komanso wakhalidwe.”

Awiriwa ali ndi mwana wa miyezi isanu dzina lake Evan.  Ukwati akuti apangitsa chaka chikudzachi koma chinkhoswe ndiye chidali pa 5 March 2017.

MarcFarlane, woyamba mwa ana atatu ndi wa kwa Chimaliro m’boma la Thyolo. Lisa, woyamba mwa ana awiri ndi wa kwa Ben Chauya ku Ntcheu.

Share This Post