Chichewa

‘Aoloka yorodani’ pamtsinje wa ruo

 

Sukulu adalekera sitandade 4, kuwerenga n’komuvuta, koma kuwerengera ndalama kwa iye si nkhani. Ngakhale sukulu sadapite nayo patali, ntchito zake zikuthandiza anthu oposa 15 000 kwa T/A Mlolo m’boma la Nsanje.

Ndi manja ake, mnyamatayu wamanga mlatho wa mamita 100 pamtsinje wa Ruo womwe anthu ambiri tsopano akuolokerapo tsiku ndi tsiku.

Mavuto atha: Ana asukulu, abizinesi ndi opita kuchipatala tsopano akutha kuoloka Ruo
Mavuto atha: Ana asukulu, abizinesi ndi opita kuchipatala tsopano akutha kuoloka Ruo

Nzoonadi, aja adati ‘wopusa adaimba ng’oma, ochenjera navina’ sadaname, tikatengera nkhani ya Laitoni Anoki, wa zaka 28, yemwe amachokera m’mudzi mwa Khasu.

Ngati ena poyamba ankamutenga ngati wopanda phindu kaamba koti sukulu adatulukira pawindo, lero wasanduka momboli wawo. Ngakhale mafumu m’derali akuvomereza kuti Anoki ndi ‘ngwazi’ ya anthu kumeneko.

Njinga zamoto, zakapalasa komanso matumba a chimanga ndi zigubu za mafuta zikuoloka pamenepa popanda vuto.

Zonse zidayamba ndi madzi osefukira amene adavuta chaka chino. Chifukwa chosefukira mtsinje wa Ruo udaiwala khwawa n’kuphotchola. Midzi yambiri idakokoloka, anthu makumimakuni adafa pangoziyo, osanena za ziweto ndi kukokoloka kwa minda.

Mtsinjewu udachititsa kuti anthu azilephera kupita kuchipatala ku Makhanga Health Centre, kusukulu yasekondale ya Makhanga, komanso kumsika wa Admarc m’derali. Mtsinjewo wachitanso malire ndi dziko la Mozambique komwe anthuwa amapitako kukasuma chimanga kutsatira njala yomwe yagwa m’bomali komanso ndiko kukuchokera mafuta ophikira.

Poyamba, anthuwa ankangoyenda osaoloka mtsinje chifukwa padalibe mtsinje. Ankaoloka Ruo pokhapo ngati akupita ku Mozambique.

Anthu a derali, kudzera mwa mafumu awo, akhala akupempha mabungwe komanso boma kudzera mwa phungu wawo Esther Mcheka Chilenje kuti awamangire mlatho pa Ruo koma kuli chuu.

“Ngoziyi itangochitika, phungu wathu adabwera kudzationa ndipo adatitsimikizira kuti atimangira mlatho poona kuti sitingathenso kupita kuchipatala ndi madera ena. Koma mpaka lero sitikudziwa kuti lonjezoli litheka liti,” adatero gulupu Manyowa.

Adadza ndi nzeru zomanga mlatho: Anoki
Adadza ndi nzeru zomanga mlatho: Anoki

Manyowa akuti anthu pafupifupi 15 000 ndiwo akhudzidwa mwa magulupu 13 onse a mwa T/A Mlolo.

Ataona kufunika kwa mlatho pamtsinjewu Anoki, ngati wamisala, adayamba kudula mitengo nayamba kukhoma mlathowo.

Pocheza ndi Msangulutso, mnyamatayu akuti adayamba ntchito yomanga mlathowu mvula ili pafupi kusiya, apo n’kuti madzi akulekeza m’khosi.

“Poona kuti ntchito indikulira ndidakopa anyamata ena kuti tithandizane. Tidalipo 8. Tidadula mitengo ndipo ina ndimachita kugula. Ndidakagula misomali, ina anthu adangotipatsa koma ina ndidachita kukongola pamtengo wa K40 000.

“Zida zitakwana, tidayamba kukhoma mitengo pamadzipa. Timasongola kaye mitengoyo ndi kukhoma ndi hamala. Ntchito idalipo chifukwa madzi n’kuti ali ambiri moti mwina amandilekeza m’khosi,” adatero Anoki.

Pakutha pa miyezi itatu, mlatho wotalika ndi mamita 100 n’kuti utatha ndipo anthu adayamba kuolokerapo.

“Ngakhale tidamaliza komabe tsiku lililonse timaugwiragwira chifukwa pena umapeza msomali wazuka kapena mtego wachoka chifukwa pamadutsa anthu ambiri,” adatero.

Lero Anoki wayamba kudyerera thukuta lake pamlathowu.

“Munthu mmodzi amalipira K100 kupita ndi kubwera. Njinga yamoto timalipitsa K200, thumba lolemera ndi makilogalamu 50 timalipitsa K100, koma opita kuchipatala sitimawalipiritsa.”

Patsiku Anoki akuti amapanga ndalama yosachepera K20 000. Sungadabwe kumuona mnyamatayu lero akutuluka m’nyumba yanjerwa zootcha komanso yamalata, ndipo wagula mbuzi zingapo, kumunda waikako aganyu.

Kupatula apo, Anoki walemba ntchito anyamata asanu kuti azithandizira pamlathowo.

“Anthu amaoloka ndi usiku womwe. Komanso pakufunika anthu olondera ndiye pali anyamata asanu amene akuthandiza. Ena amathandizira kuolotsa njinga. Patsiku ndikumawalipira K1 500 aliyense,” adatero Anoki.

Anyamata amene adamanga nawo mlathowu akulandiranso zawo. “Chomwe tapanga n’kuti tizigawana sabata yolandira ndalamazi. Sabata ino ndilandira ndineyo, ndiye kuti wina alandira sabata yamawa.”

“Mmene tikuteremu ndiye kuti ndalama yokonzetsera mlathowu imakhalanso tasunga. Mukuona anthu akubweretsa mitengo, amenewa tikufuna tiwagule kuti zida zikhale zokwanira,” adatero Anoki, uku akusintha ndalama zopatsa kasitomala.

Mphindi 20 zomwe tidakhala pamlathowo, onyamula zigubu za mafuta ndi matumba a chimanga kuchokera m’dziko la Mozambique, opita kuchipatala komanso ophunzira ndi alimi ndiwo amaoloka mowirikiza.

Lero dzina la Anoki silisowanso m’mudzimo. Gulupu Manyowa akuti alibe naye mawu mnyamatayu.

“Mtsinje umenewu ndi waukulu, anthu 9 a m’mudzi mwanga adapita akuoloka mtsinjewu. Lero tikutha kumaoloka mwaufulu, zomwe sitidaziganize chifukwa maso anthu adali kuboma. Izi zidatipatsa chimwemwe.

“Pano tikumapita kumsika, kusekondale, ku Mozambique komanso ku Admarc mopanda vuto. Simungapite ku Bangula kuchokera kuno osadutsa pamlathowu,” adatero Manyowa amene akuti masiku ena samalipitsidwa.

Mkulu wina amene ankapita kuchipatala ndi bambo ake adati mlathowu wawathandiza kopambana.

Mkuluyu, Gift Filipo, wa m’mudzi mwa James kwa Gulupu Mchacha, akuti pachipanda mlathowu sakadapita ndi bambo ake kuchipatalako.

“Tikudutsa pomwepa kupita ku Chilomo kapena Mtengera m’dziko la Mozambique. Mlathowu ukutithandiza chifukwa Ruo alibe mlatho kuno,” adatero. n

 

 

Related Articles

Back to top button