Aonjezera masiku a katemera

Mkulu wa oyang’anira zaumoyo mu unduna wa zaumoyo Dr Charles Mwansambo wati ngakhale ntchito yopereka katemera wa chikuku wa Rubella idayenda bwino, padali mavuto ena amene adachititsa kuti aonjezera masiku opereka katemerayo.

Kuyambira pa 12 mpaka 16 June, boma lidapereka katemerayu ndipo ngakhale padali mavuto ena, ntchitoyo idayenda bwino.

“Ntchito iliyonse imakhala ndi zokolakola moti padali mavuto ena amene adachititsa kuti ana ena asabaidwe. Izi zidachititsa kuti tionjezere ndalama ndi nthawi ya katemerayu,” adatero Mwansambo.

Iye adaonjeza kuti katemerayo ndi wofunika kwambiri.

Mkulu wa bungwe la zaumoyo la Malawi Health Equity Network (Mhen) George Jobe adati ndiwokhutira ndi momwe ntchitoyo idayendera.

Iye adati: “Ntchito idayenda bwino kwambiri moti tiyamike magulu onse omwe adatengapo mbali kuti adagwira ntchito yotamandika chifukwa ameneyu ndi katemera ofunika kwambiri.”

Malingana ndi mneneri wa unduna wa zaumoyo, Adrian Chikumbe, sitalaka ya aphunzitsi imene idaliko sabata yatha idapereka mpata kwa ana omwe amangokhala kuti apite kukalandira katemerayu mwaunyinji.

“Zidachitika ngati kutulo. Chikonzero chathu chidali chopereka katemera kwa ana pafupifupi 8 miliyoni ndipo pofika Lachitatu sabata ya katemerayo, ana 80 pa 100 aliwonse adali atabayitsa,” adatero Chikumbe.

Potengera chiwerengero chomwe adapereka Chikumbe, zikutanthauza kuti m’masiku atatu okha a katemerayu, ana 6.4 miliyoni mwa ana 8 miliyoniwo adali atalandira kale katemerayo ndipo ana 1.8 miliyoni ndiwo amayenera kulandira katemera m’masiku awiri otsalira.

Chikuku (Rubella) ndi nthenda yomwe imagwira yopumira ndipo imatulutsa zidzolo m’thupi lonse ndi zizindikiro za chimfine monga kutentha thupi, kuchucha mamina ndi kutsokomola ndipo imafala popatsirana kudzera mumpweya.

Malingana ndi tsamba la zaumoyo la pa internet, chikuku (Rubella) chimayamba ndi kachilombo ka mtundu wa virus komwe n’kovuta kuthana nako kwake kotero, mwana akadwala, amayenera kupatsidwa mpata wokwanira wopuma kuti asamasewere ndi anzake.

Tsambali likusonyezanso kuti ana 90 mwa 100 omwe sadalandire katemera amakhala pachiopsezo chotenga matendawa. Izi zimachititsa unduna wa zaumoyo kukhazikitsa nyengo ya katemerayu.

Share This Post