Pamene nkhani za njala zikuyala nthenje, mayi wina ku Neno wa zaka 28 zakubadwa waotcha mwana wake m’manja chifukwa anadya mkute osapempha mayiyo.
Mkulu wapolisi ya Zalewa, Bravo Chiperesa wati mayiyo amusiya atamulangiza kuipa kochitira ana nkhanza chifukwa banja la mayiyo lidatha ndipo ali ndi ana atatu amene akadavutika akapitiriza kumuzenga milandu.
Malinga ndi Chiperesa, mayiyo, Sophia Dankeni, amamuganizira kuti adafumbatitsa mwanayo makala a moto m’manja ngati chilango atadya mkute omwe mayiyo anasunga kuti mwanayo ndi abale ake adye nthawi ina koma iye anadya yekha kaamba ka njala.
“Anthu ena a chifundo ndiwo adatengera mwanayo kupolisi koma titaona kukula kwa mabalawo tidati apite kaye kuchipatala ndipo tidadikira kuti tione zikhala bwanji,” adatero iye.
Anthu ena amene analipo panthawi yomwe mwanayu amatengeredwa kupolisi adali okwiya kwambiri ndizomwe mayiyu adapanga ponena kuti njala si chinthu chokwanira kuti mayiyu akaotchere mwana wake.