Nkhani

Apalamula poitana T/A kumwambo pafoni

Mwambo wobzala mitengo ku Bula m’boma la Nkhata Bay udasokonekera Lachinayi pamene mfumu yaikulu M’bwana idakana kupita kumwambowu ati kaamba koti okonza mwambowo sadatsate dongosolo loitanira mfumu.

Mwambowu, womwe adakonza ndi a nthambi ya zankhalango mogwirizana ndi bungwe la Temwa, udaima ndi pafupifupi mphindi 30.Mobile_phone

Apatu nkuti akuluakuluwo akukambirana za tsogolo la mwambowo ndi wapampando wa chitukuko kumeneko, Ivol Nyirenda, yemwe adabweretsa uthengawo.

Mlendo wolemekezeka pamwambowo, yemwe ndi wapampando wa khonsolo ya Nkhata Bay, Hastings Mkandawire, pamodzi ndi akuluakulu ena a boma, adangoti kakasi kusowa chochita poti zawo zinali zitada.

Nawo ana asukulu pamodzi ndi anthu ena onse oitanidwa adali nyominyomi pamalopo, pomwe ena adangokhala pansi kudikira za zotsatira za zokambiranazo.

Uwutu udali mwambo waukulu wokhazikitsa nyengo yobzala mitengo m’chigawo cha kumpoto.

Koma nkhope za anthuwo zidawala patatha mphindi 30 pomwe adaona T/A M’bwana ikutulukira m’galimoto ya mtundu woyera. Mukucheza kwathu ndi M’bwana, mfumuyi idakana kukambapo zambiri pankhaniyo ati pokana kuwaika m’mavuto omwe adakonza mwambowo.

“Afunseni omwe akonza mwambo uno, ndikayankha ine, ndingawaike m’mavuto,” idatero mfumuyo.

Koma Mkandawire, yemwe adabweretsa uthengawo, adati anthuwo sadatsate dongosolo poitana mfumuyo kumwambowo.

“Simungaitane mfumu kumwambo ngati uno kudzera palamya,” iye adatero.

Ndipo polankhulapo, mmodzi mwa okonza mwambowo, woimira DC wa boma la Nkhata Bay, Mzondi Moyo, adati zoti dongosolo silidatsatidwe sizidali zoona.

“A kunthambi ya zankhalango adatsata dongosolo poitana mfumuyi komanso tidapereka udindo woitana mfumuyi kwa a bungwe la Temwa omwe amakhala nayo pafupi kwambiri,” adatero Moyo.

Mitengo yokwana pafupifupi 8 miliyoni ibzalidwa chaka chino m’nyengo yobzala mitengo m’chigawochi.

Related Articles

Back to top button