Apayoniya akana zionetsero

Amene adali a Malawi Young Pioneers (MYP) omwe atha miyezi 10 akubindikira ku Lilongwe kufuna ndalama zawo zopumira pantchito ndipo adatsimikiza zokachita nawo zionetserozi adasintha maganizo kutatsala tsiku limodzi kuti ziwonetsero zichitike.

Mtsogoleri wa gulilo Franco Chilemba adati ganizo lochita nawo zionetserozo ngati gulu lidabwera pogwirizana ndi mfundo komanso khumbo lokapereka madandaulo kwa mtsogoleri wa dziko Peter Mutharika.

“Tidaona kuti anzathuwa adapanga njira yabwino yoti mwina n’kuyankhidwa msanga ndiye poti nafe tikufuna yankho msanga, tidaona kuti mwayi wathu udali omwewu,” adatero Chilemba.

Iye adati kutsatira zokambirana za pakati pa gululo ndi akuluakulu oyendetsa za chuma cha boma komanso malipiro a anthu opuma pa ntchito, gululo lidasintha maganizo ake ochita nawo zionetsero.

“Tidakumana ndi akuluakulu omwe akuyendetsa nkhani yathu ndipo alonjeza kuti atipangira zomwe timafuna zija moti kuyambira pa 30 April, 2018 tikhala tikuyenda m’maboma osiyanasiyana kuchita kalembera wa mamembala anthu enieni,” adatero Chilemba.

Ndondomeko ya gululo ikusonyeza kuti kuyambira pa 30 April, gulu lina lidzayambira ku Chitipa n’kukathera ku Mchinji, lina ku Ntchisi n’kukathera ku Lilongwe ndipo lina ku Mangochi mpaka ku Blantyre kuti mamembala awo alandire ndalama zawo.

Share This Post