Nkhani

Apha mwana atasemphena za ndalama

Listen to this article

Apolisi m’boma la Mangochi amanga ndi kutsekera m’chitokosi mayi wa zaka 28 chifukwa chomuganizira kuti wapha mwana wake wa zaka ziwiri atasemphana ndi mwamuna wake pa nkhani za ndalama.

Wachiwiri kwa mneneri wa apolisi m’boma la Mangochi Amina Tepani Daudi wati boma likuganizira mayiyo, Tamara Chirambo, kuti adapha mwana wake, Thomas Harawa Junior, ndipo onse ochokera m’mudzi mwa Mwakhwawa m’dera la mfumu yaikulu Wasambo m’boma la Karonga.

Daudi: Adakangana za ndalama

Malingana ndi Daudi nkhaniyo idachitika usiku wa pa 12 June chaka chino m’mudzi mwa Ng’ombe m’dera la mfumu yaikuru Namabvi ku Mangochi.

“Mayiyo ndi mkazi wachiwiri kwa msodzi wa nsomba, Thomas Harawa wa zaka 46 ndipo akhala akukhala limodzi pa doko la Ng’ombe.

“Patsikulo, banjalo lidakangana pankhani za ndalama ndipo zotsatira zake ndewu idabuka pakati pa awiriwa zomwe zidapangitsa kuti mwamunayu athawire kunyumba kwa mchimwene wake kukafuna malo obisala pa msika wa Makawa m’bomalo,” adatero Daudi.

Iye adati mbandakucha wa tsikulo, mwamunayo adalandira lamya kumudziwitsa kuti mwana wake wamwamuna wamwalira ndipo apolisi adathamangira kumaloko atadziwa izo.

Zotsatira za kuchipatala chachikulu cha Mangochi zidaonetsa kuti mwanayu adamwalira chifukwa chopotokoledwa khosi.

Mayiyo akaonekera kubwalo la milandu posachedwapa komwe akayankhe mlandu wokupha.

Pakadali pano apolisi m’bomalo apempha anthu kuti apewe kutengera malamulo m’manja mwawo akasemphana pankhani za m’banja koma azikauza ankhoswe a mabanja awo kapena kupita kuma ofesi apolisi yoona za chinsinsi (Victim Support Unit) kukakambilana modekha.

Related Articles

Back to top button