ChichewaEditors Pick

Aphungu adzuma ndi kagawidwe ka makuponi

Listen to this article

Ganizo la boma loyamba kugawa makuponi ogulira zipangizo za ulimi zotsika mtengo mupologalamu ya sabuside lalandilidwa ndi maganizo osiyanasiyana pakati pa aphungu a ku Nyumba ya Malamulo, mafumu ndi Amalawi ena.

Kauniuni wa Tamvani wapeza kuti pomwe boma lili ndi maganizo oyamba kugawa makuponiwa m’chigawo cha kummwera, anthu ali ndi maganizo ena makamaka polingalira kuti mvula ili pakhomo m’zigawo zonse.

Lachinayi lapitali mudali chisokonezo m’Nyumba ya Malamulo ku Lilongwe pomwe aphungu amafuna kuti boma lilongosole momveka bwino cholinga choyamba kugawa makuponi kummwera.

Nkhani inakula m’Nyumba ya Malamulo ndi ya makuponi
Nkhani inakula m’Nyumba ya Malamulo ndi ya makuponi

Phungu wa kumadzulo kwa boma la Mzimba Harry Mkandawire ndiye adatokosa nkhaniyi ponena kuti anthu a m’boma lake akufunika makuponi ogulira zipangizo zaulimi msanga chifukwa mvula idagwa kale ndipo anthu akudikira kudzala.

“N’chifukwa chiyani mwasankha kuyambira kummwera pomwe mvula yayamba kale m’maboma ambiri m’zigawo zonse? Pamenepa pali mafunso ambiri ofunika mulongosole bwino,”adatero Mkandawire.

adakhazikike, aphungu ambiri adaimirira pofuna kuonetsa kusakhutira kwawo ndi ganizoli mpaka nduna ya zachuma Goodall Gondwe, yemwe amayankha mmalo mwa nduna ya zamalimidwe, Allan Chiyembekeza, adavomereza kuti ndondomeko ya sabuside idalakwika.

Gondwe adati ganizo loyamba kugawa makuponi ku mmwera lidadza polingalira kuti nthawi zambiri mvula imayambira m’chigawochi pakudza.

“Si kuti pali mangawa alionse, ayi, koma monga tikudziwa, chaka ndi chaka mvula imayambira kummwera ikamabwera n’chifukwa tidaganiza zoyambira kumeneko,” adatero Gondwe.

Yankholi silidagwire mtima aphunguwo ndipo adadzudzula boma chifukwa cholephera kukonzekera mokwanira mupologalamuyi.

Mkulu wa mgwirizano wa mabungwe omwe amakhudzidwa ndi nkhani za ulimi wa Civil Society Agriculture Network (Cisanet) Tamani Nkhono-Mvula adati ngakhale kuti n’chizolowezi kuyambira kummwera kugawa makuponi, chaka chino chokha ndondomeko ikadasintha.

Iye adati boma lachedwa pachilichonse mundondomekoyi ndiye sipakufunika kutsatira za mmbuyo koma kupeza njira zomwe zingagwirizane ndi momwe zinthu zilili.

“Chiyambireni, boma silidakonzekere bwino ndondomekoyi. Pena pake tikhoza kuwamvetsetsa kuti pali mavuto a zachuma koma adadziwa kalekale zimenezi ndipo pano amayenera kukhala ndi njira,” adatero Mvula.

Iye adati chomwe boma likadachita nkuthamangitsa chilichonse kuti makuponi afikire m’madera onse kuti mvula ikamayamba alimi asadzazingwe nthawi yothaitha.

“Akuganiza bwanji poti nthawi yatha kale? Mavuto a zachuma ali apo, akadapanga zoti makuponi apezeke msanga ndipo anthu alandire mzigawo zonse msanga.

“Kunjaku kuli kale njala ndipo ngati sitisamala, chaka cha mawa kukhoza kudzakhala zovuta zenizeni chifukwa alimi ambiri amadalira sabuside ndipo mmadera momwe anthu amalima kwambiri, mvula idagwa kale koma sali ku mmwera,” adatero Mvula.

Paramount Chief Lundu wa m’boma la Chikwawa adati m’madera ambiri m’chigawo cha pakati mvula idagwa kale ndipo anthu akungoyembekeza kubzala.

Iye adati kuchedwetsa makuponi kupangitsa kuti anthu adzalandire mochedwa zomwe zingachititse kuti mbewu zawo zidzasemphane ndi mvula monga momwe zidalili chaka chatha.

“Akadangoti tochepa tomweto agawe dziko lonse kuti m’zigawo zonse anthu ena abzaleko osati m’chigawo chimodzi chokha chifukwa sitikudziwanso kuti makuponi enawo afika liti ndipo adzafika angati,” adatero Lundu.

Paramount Chief Kyungu wa ku Karonga adati kwa iye nkhani yaikulu padakalipano ndi chakudya osati makuponi monga momwe anthu ena akunenera.

Iye adati mvula sidanunkhire m’maboma ambiri m’chigawochi ndiye palibe kanthu komwe angayambire chachikulu anthu apeze chakudya basi,” adatero Kyungu.

T/A Mkanda wa ku Mulanje adati iye ndi wokondwa kuti makuponi afika tsopano m’dera lake ndipo akudikira kuti mvula ikagwa anthu akabzale mbewu m’minda mwawo.

Unduna wa zamalimidwe udalengeza kuti makuponi ochepa okha ndiwo adafika m’dziko muno ndipo ayambira kugawidwa kummwera. n

Related Articles

Back to top button