Chichewa

Aphungu avuta

Listen to this article

 

Tsikulo pa Wenela padali ziii! Moti ojiya, osolola ndi osenza onse adali khumakhuma. Ndalamatu, ndalama zalowa ku silent ndiye anthu sakuyenda.

Basi ya Lilongwe imatenga tsiku lonse kuti idzadze. Ambirinso amachita kunenerera. Nchifukwa chake ndidangoganiza zolowera malo aja timakonda pa Wenela.

Ndidakapeza Abiti Patuma ndi Gervazzio akumvera nyimbo ya Lucius.

Poti sitima, imaphweka akamayendetsa wina….

Sindikudziwa kuti nyimboyo adaika chifukwa chiyani!

Abiti Patuma adali bize pafoni yake.

art

“Koma abale, phungu uyunso ndiye amangokhalira pa Facebook. Taonani lero akuti iye sakufuna kukwezeredwa ndalama. Ndidakuuzani kale kuti uyu wokonda kuvina kanindoyu amangofuna kuti anthu azimumvera.

Mwaiwala zija ankanena zolodza azungu osakaza la Mulanje phiri; mwamuiwala kuti ngwanthabwala basi?” adatero Abiti Patuma.

“Zoona. Chomwe ndikudabwa nchakuti kodi bwanji phunguyu akutokota pa Facebook mmalo mwa pagulu la aphungu anzake? Ndikuona ngati nzeru zikumuchepera kapena Chingerezi ndiye vuto kwa regisrator (sic) ameneyu,” adayankhira Gervazzio.

Abale anzanga, kunena zoona wamisala adaona nkhondo. Vuto limakhala lakuti iye sadathawe, adakhala limodzi ndi anthu ena m’mudzimo. Iyetu adafera limodzi ndi ena onse.

“Kodi iyeyo ngakhale akulankhula pa Facebook kuti anthu amutamandire, malipiro atakwezedwa iyeyo angakane? Chiphimbam’maso ichi basi,” ndidailowerera.

Koma zonse zili apo, aphunguwa akutionjeza pano pa Wenela. Ndalamatu zalowa ku silent ndiye wina azifuna mamiliyoni pamwamba pa mamiliyoni anzake.

“Ndiye ndinamva wina akunena kuti amalandira zosaposa K250 000. Bodza inu! Momwe anthu awa amayendera, kumalandira maalawansi ochuluka aziti akulandira zochepa? Anthu awa Mulungu adzachititse nthaka iwameze tsiku lina,” adatero Abiti Patuma.

Usiku wa tsikulo ndidalota maloto odabwitsa. Ndidalota nditapita ku Nyumba ya Malamulo ngati mlendo wa phungu wathu pa Wenela, Mr Water Bouncer, mzungu wathu.

Kutuloko ndidaona kuti nyumbayo idapita patsogolo kwambiri. Adali kulankhula ndi phungu wina amene adakhalapo msirikali woimba mabatcha.

“Indetu ndinena ndi inu aphungu anzanga. Dziko lafika pena. Tatukuka. Onani tili ndi ma tablet, ma laptop, mafoni a touch ndi zida zina koma tikulephera kuzigwiritsa bwino ntchito. Kulibe Wi-fi,” adali kutero mkulu wathupi lakeyo.

Musandifunse kuti Wi-fi nchiyani chifukwa sindingakuuzeni. Nanga ndichite kukuuzani kuti ndi njira imene anthu angalumikizire makina ndi mafoni awo ku Internet popanda chingwe?

“Ndimayesatu tsitsi la mbuu ndi mgodi wa nzeru, koma apa zikuoneka ndi zina. Mukalandira ndalama zankhaninkhani tsono mukufunanso Internet yaulere? Mmalo moti mumenyere ufulu kuti Internet ikhale yaulere kwa ana asukulu! Mubwereratu koimba mabatcha kuusirikali,” adamuyankha phungu wina.

Ndidadzidzimuka.

Gwira bango, upita ndi madzi mwaiwe!

Related Articles

Back to top button
Translate »