Nkhani

APM akuzemba PAC —Akatswiri a ndale

Listen to this article

Othirira ndemanga pa ndale m’dziko muno ati zimene mtsogoleri wa dziko lino Peter Mutharika wachita posakumana ndi a bungwe la Public Affairs Committee (PAC) kuti amve zomwe msonkhano wawo udagwirizana pa za mmene zinthu zilili m’dziko muno zikuonetsa kuti mtsogoleriyu akuzengereza dala kuti nkhaniyi izizire ndi kuiwalika.

Aphunzitsi awiri a kusukulu ya ukachenjende ya Chancellor College omwenso ndi anamatetule pa nkhani za ndale, Boniface Dulani ndi Joseph Chunga anena izi m’sabatayi pothirapo ndemanga pa kulephereka kwa mkhumano wa akuluakulu a bungweli ndi mtsogoleriyu.

Akuti mpata sakuupeza: Mutharika
Akuti mpata sakuupeza: Mutharika

Kawiri konse Mutharika wasintha nthawi yokumanirana ndi akuluakulu a PAC ponena kuti ndi wotanganidwa ndi ntchito zina.

Poyankha PAC imayembekezera kukumana ndi Mutharika pa 25 February koma zidakanika ndipo boma lidati mkhumanowu uchitika pa 29 March zomwenso zalephereka.

Mkulu wa bungweli la PAC Robert Phiri wati iwo adafika mumzinda wa Blantyre kuti akumane ndi Mutharika koma mwadzidzidzi adangomva kuti nkhumanoyo yalephereka.

Izi zachititsa kuti PAC ilephere kufotokozera Mutharika zomwe msonkhano wawo, womwe udachitika pa 17 February chaka chino, udagwirizana.

Koma akadaulowa akuganiza kuti Mutharika akungozemba chabe osati watanganidwa ndipo ati izi sizingachitire ubwino anthu amene akuyembekezera mayankho pa mfundo zomwe zikukhudza Amalawi.

Dulani adati zomwe akuchita Mutharika ndi kuzemba chabe n’cholinga choti nkhani zomwe zidatuluka ku PAC zizizire ndi kuiwalika.

“Akungozemba chabe. Inde, Pulezidenti amakhala wotangwanika, koma sindikukhulupirira kuti angalephere kupeza nthawi yokumana ndi a PAC.

“Chomwe tingadziwe, dziko lino lili pamavuto aakulu kotero tikuyenera kupeza mayankho mwachangu ndipo izi ndi zomwe bungwe la PAC lidachita kumva maganizo kwa anthu osiyanasiyana,” adatero Dulani.

Koma mneneri wa boma, Jappie Mhango, wati si zoona kuti Mutharika akuzemba, koma kuti mtsogoleriyu amakhala wotanganidwa ndi ntchito zambiri.

“A Pulezidenti amayeneradi kukumana ndi a PAC koma sizidatheke chifukwa cha nkhumano zinazo zomwe akuyenera akakhalepo, koma si kuti akuthawa, ayi,” adatero Mhango.

Mhango wati tsiku lomwe akumane ndi akuluakulu a PAC awadziwitsa akuluakuluwa koma izi zichitika Mutharika akakhala ndi mpata wotero.

Kadaulo wina pandale ku Chancellor  College, Joseph Chunga, wati Mutharika ali ndi nthawi yambiri yomwe angakwanitse kukumana ndi PAC koma izi zikungoonetsa kuti sakufuna.

“Ndikuganiza kuti mtsogoleriyu akungofuna kugula nthawi kuti akonze zomwe PAC idakambirana n’cholinga choti pamene azikumana nawo akhale atakonza zinthu zina,” adatero Chunga.

Chunga watinso Mutharika adauzidwa kale ndi akuluakulu a boma amene adali nawo pamsonkhanowo za zomwe adakambirana.

“Si kuti sakudziwa zomwe zidakambidwa, zidali m’manyuzipepala komanso nduna zake zikuyenera kuti zidamufotokozera, komabe ngakhale izi zili chonchi, akuyenera kukumana ndi a PAC chifukwa ndi oima paokha,” adaonjeza.

Msonkhano wa PAC mwa zina udagwirizana kuti Mutharika akonze zinthu pano. Izi ndi monga kusowa kwa chimanga. Zinanso zomwe adagwirizana nkuti boma lichotse zinthu zina zomwe likuchita pofuna kupeza mavoti monga kukweza mafumu ndi pologalamu yomangira anthu nyumba ya Cement and Malata Subsidy.

Mfundo ina, PAC idatinso Mutharika akuyenera kukwaniritsa mfundo zonse zomwe adalonjeza kuti achita akalowa m’boma ponena kuti zaka ziwiri zomwe wakhala akulamula n’zambiri.n

Related Articles

Back to top button